-
Yeremiya 32:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Pa nthawi imeneyo, asilikali a mfumu ya Babulo anali atazungulira Yerusalemu. Ndipo mneneri Yeremiya anali atamutsekera mʼnyumba imene inali mʼBwalo la Alonda,+ limene linali pafupi ndi nyumba ya mfumu ya Yuda.
-
-
Yeremiya 37:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Choncho Mfumu Zedekiya inalamula kuti Yeremiya atsekeredwe mʼBwalo la Alonda+ ndipo tsiku lililonse ankamupatsa mtanda wozungulira wa mkate.+ Mkate umenewu unkachokera kumsewu wa ophika mkate ndipo anapitiriza kumʼpatsa mkatewo mpaka mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala mʼBwalo la Alonda.
-