-
Yeremiya 41:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye atamva zoipa zonse zimene Isimaeli mwana wa Netaniya anachita,
-
-
Yeremiya 41:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ndiyeno Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye anatenga anthu onse amene anatsala ku Mizipa. Anthu amenewa ndi amene anawapulumutsa mʼmanja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Anapulumutsa amuna, asilikali, akazi, ana ndi nduna zapanyumba ya mfumu ndipo anabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni.
-
-
Yeremiya 43:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Azariya mwana wa Hoshaya, Yohanani+ mwana wa Kareya ndi anthu onse odzikuza anauza Yeremiya kuti: “Zimene ukunenazo ndi zabodza! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti udzatiuze kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko.’
-