-
Hoseya 2:12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi ya mkuyu imene iye wanena kuti:
“Amenewa ndi malipiro amene amuna ondikonda kwambiri anandipatsa.”
Koma ine mitengoyo ndidzaisandutsa kukhala nkhalango,
Ndipo zilombo zakutchire zidzaidya.
-
-
Mika 1:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Zifaniziro zake zonse zogoba zidzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswazidutswa.+
Ndipo mphatso zonse zimene ankalandira ngati malipiro zidzatenthedwa pamoto.+
Mafano ake onse ndidzawawononga.
Chifukwa anawapeza kuchokera ku ndalama zimene ankalandira pochita uhule.
Ndipo tsopano zinthu zimenezi zidzatengedwa kuti zikakhale malipiro a mahule kwinakwake.”
-