-
2 Mafumu 15:32-34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Mʼchaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, Yotamu+ mwana wa Uziya+ mfumu ya Yuda anakhala mfumu. 33 Yotamu anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 34 Iye ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira bambo ake Uziya.+
-
-
2 Mbiri 27:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Yotamu+ anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 16. Mayi ake dzina lawo linali Yerusa mwana wa Zadoki.+ 2 Yotamu ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Uziya bambo ake,+ kungoti sanachite makani nʼkukalowa mʼkachisi wa Yehova.+ Koma anthu ankachitabe zoipa.
-