Salimo
137 Tinakhala pansi mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo.+
Tinalira titakumbukira Ziyoni.+
3 Chifukwa kumeneko, anthu amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+
Amene ankatinyozawo ankafuna kuti tiwasangalatse. Iwo anati:
“Tiimbireni nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.”
4 Tingaimbe bwanji nyimbo ya Yehova
Mʼdziko lachilendo?
5 Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,
Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.+
6 Lilime langa limamatire mʼkamwa mwanga
Ngati sindingakukumbukire,
Ngati sindingaike Yerusalemu pamwamba
Pa chilichonse chimene chimandisangalatsa kwambiri.+
7 Inu Yehova, kumbukirani
Zimene Aedomu ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa.
Iwo anati: “Gwetsani mzindawo! Ugwetseni mpaka pamaziko ake!”+
8 Iwe mwana wamkazi wa Babulo,* amene watsala pangʼono kuwonongedwa,+
Wosangalala adzakhala amene adzakubwezere
Zimene iwe watichitira.+
9 Wosangalala adzakhala amene adzagwire ana ako
Nʼkuwaphwanya powawombetsa pathanthwe.+