Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • es25
  • October

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • October
  • Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
  • Timitu
  • Lachitatu, October 1
  • Lachinayi, October 2
  • Lachisanu, October 3
  • Loweruka, October 4
  • Lamlungu, October 5
  • Lolemba, October 6
  • Lachiwiri, October 7
  • Lachitatu, October 8
  • Lachinayi, October 9
  • Lachisanu, October 10
  • Loweruka, October 11
  • Lamlungu, October 12
  • Lolemba, October 13
  • Lachiwiri, October 14
  • Lachitatu, October 15
  • Lachinayi, October 16
  • Lachisanu, October 17
  • Loweruka, October 18
  • Lamlungu, October 19
  • Lolemba, October 20
  • Lachiwiri, October 21
  • Lachitatu, October 22
  • Lachinayi, October 23
  • Lachisanu, October 24
  • Loweruka, October 25
  • Lamlungu, October 26
  • Lolemba, October 27
  • Lachiwiri, October 28
  • Lachitatu, October 29
  • Lachinayi, October 30
  • Lachisanu, October 31
Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku—2025
es25

October

Lachitatu, October 1

Nzeru yochokera kumwamba . . . ndi . . . yokonzeka kumvera.​—Yak. 3:17.

Kodi nthawi zina zimakuvutani kukhala omvera? Zimenezi zinkachitikiranso Mfumu Davide. Choncho iye anapemphera kwa Mulungu kuti: “Ndipatseni mtima wofunitsitsa kukumverani.” (Sal. 51:12) Davide ankakonda Yehova. Komabe, nthawi zina iye ankavutika kumvera ngati mmenenso zimakhalira ndi ifeyo. Chifukwa chiyani? Choyamba, tinatengera mtima wosafuna kumvera. Chachiwiri, nthawi zambiri Satana amachititsa kuti tisamvere Yehova ngati mmene iyeyo anachitira. (2 Akor. 11:3) Chachitatu, tikukhala m’dziko limene anthu ali ndi ‘kaganizidwe kamene tsopano kakugwira ntchito mwa ana a kusamvera.’ (Aef. 2:2) Tizichita khama kuti tizitha kulimbana ndi mtima wofuna kuchita tchimo komanso kupewa zimene Mdyerekezi ndi anthu a m’dzikoli amatilimbikitsa kuchita kuti tikhale osamvera. Tiyenera kuyesetsa kuti tizimvera Yehova komanso anthu amene wawasankha kuti azititsogolera. w23.10 42:1

Lachinayi, October 2

Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.​—Yoh. 2:10.

Kodi tikuphunzira chiyani pa chozizwitsa cha Yesu chosandutsa madzi kukhala vinyo? Tikuphunzirapo khalidwe la kudzichepetsa. Yesu sanadzitame chifukwa cha chozizwitsa chomwe anachita ndipotu sanadzitamepo pa zonse zomwe anachita. M’malomwake, modzichepetsa komanso mobwerezabwereza, ankapereka ulemerero wonse kwa Atate wake. (Yoh. 5:19, 30; 8:28) Tikamatsanzira Yesu pokhala odzichepetsa, sitingamadzitame chifukwa cha zimene takwanitsa kuchita. Choncho kaya tikuchita zotani potumikira Yehova, tisamadzitame chifukwa cha zimene tikuchitazo koma tizidzitama chifukwa choti tili ndi mwayi wotumikira Mulungu yemwe ndi wodabwitsa. (Yer. 9:23, 24) Tiyeni tizimupatsa ulemerero umene timayenera kumupatsa. Ndipotu palibe chabwino chilichonse chomwe tingachite popanda kuthandizidwa ndi Yehova. (1 Akor. 1:26-31) Tikakhala odzichepetsa sitingafune kuti anthu azitilemekeza chifukwa cha zabwino zomwe tachitira ena. Timakhala okhutira chifukwa chodziwa kuti Yehova amaona komanso kuyamikira zimene timachita. (Yerekezerani ndi Mateyu 6:2-4; Aheb. 13:16) Ndipotu timasangalatsa Yehova tikamatsanzira Yesu pokhala odzichepetsa.—1 Pet. 5:6. w23.04 15:9, 11-12

Lachisanu, October 3

Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.​—Afil. 2:4.

Mouziridwa, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuti aziganiziranso zofuna za ena. Kodi tingagwiritse ntchito bwanji malangizo amenewa pamisonkhano? Tizikumbukira kuti mofanana ndi ifeyo, enanso akufuna kuyankha. Taganizirani izi: Pamene mukucheza ndi anzanu, kodi mumangolankhula nokha osawapatsako mpaka woti alankhulepo? Ayi, simungachite zimenezo. Mumafuna kuti nawonso azilankhulapo. Mofanana ndi zimenezi, pamisonkhano timafuna kuti anthu ambiri azipereka ndemanga. Ndipotu imodzi mwa njira zabwino kwambiri zolimbikitsira abale ndi alongo athu ndi kuwapatsa mpata woti afotokoze zokhudza chikhulupiriro chawo. (1 Akor. 10:24) Mwa zina, tingapereke ndemanga yachidule, zomwe zingapereke mpata kwa ena kuti ayankhepo. Ngakhale pamene yankho lanu lili lalifupi, muzipewa kutchula mfundo zambiri. Ngati mutatchula mfundo zonse za mundime, anthu ena angasowe zoti alankhulepo. w23.04 18:11-13

Loweruka, October 4

Ndimachita zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndilalikire uthengawu kwa anthu ena.​—1 Akor. 9:23.

Tiyenera kukumbukira kuti chofunika kwambiri ndi kuthandiza ena, makamaka pogwira nawo ntchito yolalikira. Tikamagwira ntchito yolalikira, tiyenera kukhala okonzeka kusintha. Timakumana ndi anthu osiyana zikhulupiriro, kochokera komanso mmene amaonera zinthu. Mtumwi Paulo ankatha kusintha akamalalikira ndipo tingaphunzirepo kanthu pa chitsanzo chake. Yesu anasankha Paulo kukhala “mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina.” (Aroma 11:13) Pa utumiki wakewu, iye ankalalikira Ayuda, Agiriki, anthu ophunzira, alimi, anthu olemekezeka ndiponso mafumu. Kuti aziwafika pa mtima, Paulo ankakhala “zinthu zonse kwa anthu osiyanasiyana.” (1 Akor. 9:19-22) Iye ankachita chidwi ndi zikhalidwe, kochokera ndiponso zikhulupiriro za anthuwo, ndipo ankasintha mmene ankalalikirira kuti zigwirizane ndi zimenezo. Ifenso zinthu zingamatiyendere bwino mu utumiki ngati timachita chidwi ndi anthu n’kumasintha mmene timalalikirira kuti zigwirizane ndi mmene zinthu zilili pa moyo wawo. w23.07 32:11-12

Lamlungu, October 5

Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu. Koma ayenera kukhala wodekha kwa onse.—2 Tim. 2:24.

Munthu akakhala wofatsa sizitanthauza kuti ndi wofooka. Pamafunika kukhala wamphamvu kuti ukhale wodekha ukakumana ndi vuto linalake. Kufatsa ndi limodzi mwa “makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera.” (Agal. 5:22, 23) Mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti “kufatsa” nthawi zina ankawagwiritsa ntchito pofotokoza za hatchi yam’tchire yomwe ikuwetedwa. Taganizirani za hatchi yam’tchire yomwe yaphunzitsidwa kukhala yodekha. Hatchiyo ingakhale yodekha, koma imakhalabe yamphamvu. Ndiye kodi anthufe tingakhale bwanji ofatsa, pa nthawi imodzimodziyo n’kukhalanso amphamvu? Sitingathe kuchita zimenezi patokha. Chomwe chingatithandize ndi kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu wake womwe ungatithandize kuti tikhale ndi khalidwe labwinoli. Pali umboni wosonyeza kuti zimenezi ndi zotheka. Abale ndi alongo ambiri amayankha mofatsa anthu otsutsa ndipo izi zimathandiza kuti anthu akhale ndi maganizo oyenera okhudza a Mboni za Yehova.—2 Tim. 2:24, 25. w23.09 39:3

Lolemba, October 6

[Ndinkapemphera] ndipo Yehova wandipatsa zimene ndinapempha.​—1 Sam. 1:27.

M’masomphenya ochititsa chidwi, mtumwi Yohane anaona akulu 24 kumwamba akulambira Yehova. Iwo ankatamanda Mulungu podziwa kuti ndi woyenera kulandira ‘mphamvu, ulemerero ndi ulemu.’ (Chiv. 4:10, 11) Angelo okhulupirika alinso ndi zifukwa zowachititsa kutamanda ndi kulemekeza Yehova. Iwo amakhala naye limodzi kumwamba ndipo anafika pomudziwa bwino kwambiri. Amaonanso makhalidwe ake kudzera m’zochita zake. Akamaona mmene Yehova amachitira zinthu, zimawachititsa kuti azimutamanda. (Yobu 38:4-7) Ifenso timafuna kutamanda Yehova m’mapemphero athu n’kumafotokoza zimene timakonda komanso kuyamikira zokhudza iye. Mukamawerenga komanso kuphunzira Baibulo, muziyesa kupeza makhalidwe ake omwe amakusangalatsani kwambiri. (Yobu 37:23; Aroma 11:33) Kenako muzimuuza Yehova mmene mukumvera chifukwa cha makhalidwewo. Tingamutamandenso chifukwa chotithandiza ifeyo komanso abale ndi alongo athu.—1 Sam. 2:1, 2. w23.05 20:6-7

Lachiwiri, October 7

Mukhale ndi khalidwe logwirizana ndi zimene Yehova amafuna.​—Akol. 1:10.

Mu 1919, anthu a Mulungu anatuluka mu Babulo Wamkulu. Pa nthawi imeneyi, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” anaikidwa ndipo inali nthawi yoyenera chifukwa iye anayamba kuthandiza anthu a mtima wabwino kuti ayambe kuyenda pa “Msewu Wopatulika,” womwe unali utangotsegulidwa kumene. (Mat. 24:45-47; Yes. 35:8) Chifukwa choti atumiki okhulupirika anali atagwira ntchito yokonza msewuwu m’mbuyomu, anthu amene ankayenda pamsewu waukuluwu, akanatha kudziwa zambiri zokhudza zolinga za Yehova. (Miy. 4:18) Akanathanso kusintha moyo wawo kuti uzigwirizana ndi zimene Yehova amafuna. Yehova sayembekezera kuti anthu ake asinthe kamodzin’kamodzi. M’malomwake, iye wakhala akuwathandiza mwapang’onopang’ono. Tonsefe tidzasangalala kwambiri pamene tizidzasangalatsa Mulungu wathu pa chilichonse. Msewu uliwonse umafunika kumakonzedwa pafupipafupi. Kungochokera mu 1919, ntchito yokonza “Msewu Wopatulika” yakhala ikupitirira n’cholinga chofuna kuthandiza anthu ambiri kutuluka mu Babulo Wamkulu. w23.05 22:15-16

Lachitatu, October 8

Sindidzakusiyani.​—Aheb. 13:5.

Abale a m’Bungwe Lolamulira akhala akuphunzitsa abale amene amathandiza makomiti osiyanasiyana a Bungwe Lolamulira. Panopa abale othandizawa akugwira mokhulupirika ntchito zambiri m’gulu la Yehova. Abalewa ndi okonzekeretsedwa kupitiriza kusamalira bwino nkhosa za Khristu. Choncho wodzozedwa womaliza akadzatengedwa kupita kumwamba kumapeto kwa chisautso chachikulu, kulambira koona kudzapitirizabe padzikoli. Motsogoleredwa ndi Yesu Khristu, atumiki a Mulungu adzapitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika. N’zoona kuti pa nthawiyo tidzaukiridwa ndi Gogi wa ku Magogi, yemwe ndi mgwirizano wa mayiko. (Ezek. 38:18-20) Koma kuukiridwa kwa kanthawi kumeneku sikudzalepheretsa anthu a Mulungu kukhalabe okhulupirika. Iye adzawapulumutsa. M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona “khamu lalikulu” la nkhosa zina za Khristu. Yohane anauzidwa kulemba kuti “khamu lalikulu” limeneli ‘linatuluka m’chisautso chachikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Choncho sitikukayikira kuti Yehova adzawateteza. w24.02 5:13-14

Lachinayi, October 9

Musazimitse moto wa mzimu.​—1 Ates. 5:19.

Kodi tingatani kuti tizilandira mzimu woyera? Tiziupempha, kuphunzira Mawu a Mulungu komanso kukhalabe m’gulu lotsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. Kuchita zimenezi, kungatithandize kukhala ndi “makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera.” (Agal. 5:22, 23) Mulungu akatipatsa mzimu wake woyera, tiyenera kusamala kuti ‘tisazimitse moto wa mzimu.’ Mulungu amapereka mzimu wake kwa anthu okhawo amene amapitirizabe kuganiza zoyenera komanso kukhala ndi makhalidwe abwino. Iye angasiye kutipatsa mzimu wake ngati timapitiriza kuganizira zinthu zoipa komanso kumazichita. (1 Ates. 4:7, 8) Kutinso tipitirize kulandira mzimu woyera, ‘tisamanyoze mawu aulosi.’ (1 Ates. 5:20) Pavesili, “mawu aulosi” akuimira mauthenga operekedwa ndi mzimu wa Mulungu kuphatikizapo okhudza tsiku la Yehova komanso kuti tsikulo lili pafupi. Nthawi zonse timakumbukira za tsikuli ndipo sitimaganiza kuti Aramagedo siidzafika mu nthawi yathu. M’malomwake, timasonyeza kuti timaliganizira popitiriza kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kutanganidwa ndi ‘ntchito zosonyeza kuti ndife odzipereka kwa Mulungu.’—2 Pet. 3:11, 12. w23.06 26:13-14

Lachisanu, October 10

Kuopa Yehova ndi chiyambi cha nzeru.—Miy. 9:10.

Monga Akhristu, kodi tiyenera kuchita chiyani ngati pachipangizo chathu chamakono pabwera chithunzi cholaula? Mwamsanga tiyenera kupewa kuchiyang’ana. Zingakhale zosavuta kuchita zimenezi ngati timaona kuti chinthu chofunika kwambiri ndi ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndipotu zithunzi zimene anthu saziona kuti ndi zolaula kwenikweni zingachititse kuti munthu akhale ndi chilakolako cha kugonana. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa zithunzi zotere? Chifukwa sitifuna ngakhale pang’ono kuti tiziganizira zachiwerewere mumtima mwathu. (Mat. 5:28, 29) Mkulu wina wa ku Thailand dzina lake David ananena kuti: “Ndimadzifunsa kuti, ‘Ngakhale kuti zithunzizi si zolaula, kodi Yehova angasangalale ngati nditapitiriza kuziyang’ana?’ Kuganiza mwa njira imeneyi kumandithandiza kuti ndisankhe zochita mwanzeru.” Kuopa kukhumudwitsa Yehova kumatithandiza kuti tizisankha zochita mwanzeru. Kuopa Mulungu ndi “chiyambi cha nzeru.” w23.06 28:12-13

Loweruka, October 11

Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati.​—Yes. 26:20.

‘Zipinda zamkati’ zingatanthauze mipingo yathu. Pa nthawi ya chisautso chachikulu, Yehova adzatiteteza monga mmene analonjezera ngati tidzapitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi abale ndi alongo athu. Choncho panopa tiyenera kuyesetsa kuti kuwonjezera pa kulola kuchita zinthu ndi abale ndi alongo athu, tiziwakondanso. Zimenezi ndi zofunika kwambiri kuti tidzapulumuke. “Tsiku lalikulu la Yehova” lidzakhala loopsa kwa anthu onse. (Zef. 1:14, 15) Nawonso atumiki a Yehova adzakumana ndi mavuto. Ngati titakonzekereratu panopa tidzatha kukhala mosatekeseka komanso kuthandiza ena. Tidzatha kupirira mavuto alionse omwe tingakumane nawo. Abale ndi alongo athu akamadzavutika, tidzachita zomwe tingathe powasonyeza chifundo komanso kuwapatsa zimene akufunikira. Ndipo tidzagwirizana ndi abale ndi alongo athu omwe tinali titayamba kale kuwakonda. Kenako Yehova adzatidalitsa potipatsa moyo wosatha m’dziko limene simudzakhalanso mavuto alionse.—Yes. 65:17. w23.07 29:16-17

Lamlungu, October 12

[Yehova] adzakupatsani mphamvu, adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika komanso adzakulimbitsani.​—1 Pet. 5:10.

Nthawi zambiri Baibulo limafotokoza za amuna omwe anali ndi chikhulupiriro cholimba. Koma si nthawi zonse pamene iwo ankadzimva choncho. Mwachitsanzo, nthawi zina Mfumu Davide ankadziona kuti anali “wamphamvu ngati phiri,” koma nthawi zina ‘ankachita mantha.’ (Sal. 30:7) Ngakhale kuti Samisoni anali ndi mphamvu zapadera mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, ankadziwa kuti popanda kuthandizidwa ndi Mulungu ‘angafooke ndi kukhala ngati anthu ena onse.’ (Ower. 14:5, 6; 16:17) Amuna okhulupirikawa ankakhala ndi mphamvu chifukwa chakuti Yehova ndi amene ankawapatsa mphamvuzo. Mtumwi Paulo nayenso ankadziwa kuti ankafunika kupatsidwa mphamvu ndi Yehova. (2 Akor. 12:9, 10) Iye ankakumana ndi mavuto monga matenda. (Agal. 4:13, 14) Nthawi zina ankavutikanso kuchita zinthu zoyenera. (Aroma 7:18, 19) Ndipo nthawi zinanso ankada nkhawa kapena kuchita mantha. (2 Akor. 1:8, 9) Komabe, pamene Paulo ankakhala wofooka m’pamenenso ankakhala wamphamvu. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Yehova ankamupatsa mphamvu zimene ankafunikira kuti apirire mavuto ake. w23.10 43:1-2

Lolemba, October 13

Yehova amaona mumtima.​—1 Sam. 16:7.

Ngati ifenso nthawi zina timavutika ndi maganizo odziona ngati achabechabe, tizikumbukira kuti Yehova ndi amene anatikoka. (Yoh. 6:44) Iye amaona zabwino mwa ife zimene eni akefe sitiziona ndiponso amadziwa mtima wathu. (2 Mbiri 6:30) Choncho tisamakayikire akamatiuza kuti ndife amtengo wapatali. (1 Yoh. 3:19, 20) Tisanaphunzire choonadi, ambirife tinkachita zinthu zimene timadziimba nazo mlandu mpaka pano. (1 Pet. 4:3) Ngakhale Akhristu okhulupirika amalimbanabe ndi mtima wofuna kuchita zoipa. Kodi inuyo mumadziimbanso mlandu? Ngati ndi choncho, dziwani kuti atumiki a Yehova okhulupirika ambiri akhala akudziimba mlandu. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo ankadzimvera chisoni akaganizira zomwe ankalakwitsa. (Aroma 7:24) N’zoona kuti Paulo analapa machimo ake n’kubatizidwa. Komabe iye anadzitchula kuti “ndine wamng’ono kwambiri pa atumwi onse” komanso “wochimwa kwambiri.”—1 Akor. 15:9; 1 Tim. 1:15. w24.03 13:5-6

Lachiwiri, October 14

Iwo anasiya nyumba ya Yehova.—2 Mbiri 24:18.

Nkhani ya Mfumu Yehoasi ikutiphunzitsa kuti tizisankha anzathu omwe angatithandize kuti tizichita zabwino. Tizisankha anthu omwe amakonda Yehova komanso amafuna kumusangalatsa. Tisamangocheza ndi anthu amsinkhu wathu okha. Kumbukirani kuti Yehoasi anali wamng’ono kwambiri poyerekezera ndi mnzake Yehoyada. Mukamasankha anzanu muzidzifunsa kuti: ‘Kodi iwo amandithandiza kuti ndizikhulupirira kwambiri Yehova? Kodi amandilimbikitsa kuti ndizitsatira mfundo zake? Kodi amakonda kulankhula za Yehova komanso choonadi chake chamtengo wapatali? Kodi amalemekeza mfundo za Mulungu? Kodi iwo amangondiuza zinthu kuti andisangalatse kapena amalimba mtima n’kundiuza zimene ndikulakwitsa?’ (Miy. 27:5, 6, 17) Kunena zoona anthu amene sakonda Yehova sayenera kukhala anzanu. Koma ngati muli ndi anzanu omwe amakonda Yehova, pitirizani kucheza nawo chifukwa azikuthandizani.—Miy. 13:20. w23.09 38:6-7

Lachitatu, October 15

Ine ndine Alefa ndi Omega.—Chiv. 1:8.

Mawu akuti alefa amapezeka kumayambiriro kwa afabeti ya Chigiriki ndipo mawu akuti omega amapezeka kumapeto. Pogwiritsa ntchito mawu akuti “Alefa ndi Omega,” Yehova anasonyeza kuti akayamba kuchita chinthu sasiya mpaka chitatheka. Atangolenga Adamu ndi Hava, Yehova anawauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi ndipo muziliyang’anira.” (Gen. 1:28) Pa nthawi imeneyi zinali ngati Yehova akunena kuti “Alefa.” Apa iye anafotokoza momveka bwino cholinga chake. Cholingacho chinali choti pakapita nthawi, ana a Adamu ndi Hava omwe akanakhala angwiro komanso omvera adzaze dzikoli n’kulikonza kukhala Paradaiso. Pa nthawi imeneyi m’pamene zikanakhala ngati wanena kuti “Omega.” Atamaliza kulenga “kumwamba ndi dziko lapansi komanso zonse zimene zili mmenemo,” ananena mawu otsimikizira kuti cholinga chake chidzatheka. Yehova ankatsimikizira kuti cholinga chake chokhudza dziko komanso anthu sichidzalephereka. Cholingachi chikanakwaniritsidwa kumapeto kwa tsiku la 7.—Gen. 2:1-3. w23.11 46:13-14

Lachinayi, October 16

Konzani njira ya Yehova! Mulungu wathu mukonzereni msewu wowongoka wodutsa m’chipululu.​—Yes. 40:3.

Ulendo wovuta wochokera ku Babulo kupita ku Isiraeli ukanawatengera Ayuda miyezi pafupifupi 4. Koma Yehova anali atalonjeza kuti adzachotsa chilichonse chomwe chinkaoneka kuti chingawalepheretse kubwerera. Kwa Ayuda okhulupirika, kubwerera ku Isiraeli kunali kofunika kwambiri kuposa chilichonse chomwe akanasiya. Chofunika kwambiri chinali chakuti zinthu zikanayambiranso kuwayendera bwino pa nkhani ya kulambira. Ku Babulo kunalibeko kachisi wa Yehova. Kunalibe guwa limene Aisiraeli akanamaperekapo nsembe zomwe zinkafunika malinga ndi Chilamulo cha Mose. Komanso kunalibe ansembe omwe akanamapereka nsembezo. Kuwonjezera pamenepo, anthu a Yehova anali ochepa kwambiri poyerekeza ndi amuna ndi akazi achikunja omwe sankalemekeza Yehova kapenanso mfundo zake. Choncho Ayuda ambiri okhulupirika ankafunitsitsa atabwerera kwawo kuti akabwezeretse kulambira koona. w23.05 22:3-4

Lachisanu, October 17

Pitirizani kuyenda ngati ana a kuwala.​—Aef. 5:8.

Timafunika mzimu woyera wa Mulungu kuti tipitirize kuchita zinthu ngati “ana a kuwala.” Chifukwa chiyani? Chifukwa si zophweka kupitiriza kukhala oyera m’dziko la makhalidwe oipali. (1 Ates. 4:3-5, 7, 8) Mzimu woyera ungatithandize kupewa maganizo a m’dzikoli kuphatikizapo nzeru za anthu komanso mfundo zimene zimasemphana ndi maganizo a Mulungu. Ungatithandizenso kuti tizichita ‘chilichonse chabwino ndi chilichonse cholungama.’ (Aef. 5:9) Njira imodzi imene tingalandirire mzimu woyera ndi kuupempha. Yesu ananena kuti Yehova “adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akumupempha.” (Luka 11:13) Komanso tikamatamanda Yehova pamisonkhano ndi Akhristu anzathu timalandira mzimu woyera. (Aef. 5:19, 20) Mzimu woyera umatithandiza kuti tizichita zinthu zimene zimasangalatsa Mulungu. w24.03 12:13-15

Loweruka, October 18

Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.​—Luka 11:9.

Kodi mukufuna muzisonyeza kuleza mtima kwambiri? Ngati ndi choncho, muzipempha Yehova kuti akuthandizeni. Kuleza mtima ndi limodzi mwa makhalidwe omwe mzimu woyera umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Choncho tizipempha Yehova kuti atipatse mzimu wake kuti tikhale ndi makhalidwe omwe umatulutsa. Ngati tikuyesedwa pa nkhani yokhala oleza mtima, tiyenera ‘kupitiriza kupempha’ mzimu woyera kuti utithandize kukhala oleza mtima. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atithandize kuti tiziona zinthu mmene iyeyo amazionera. Kenako pambuyo popemphera, tizichita zomwe tingathe kuti tizikhala oleza mtima tsiku lililonse. Tikamapemphera kwambiri kuti tikhale oleza mtima n’kumayesetsa kusonyeza khalidweli, m’pamenenso limakhazikika kwambiri mumtima ndipo limangokhala ngati mbali ya moyo wathu. Chinanso chomwe chingatithandize ndi kuganizira mozama za anthu otchulidwa m’Baibulo. M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu omwe anali oleza mtima. Tikhoza kuphunzira mmene tingasonyezere kuleza mtima tikamaganizira kwambiri zitsanzozi. w23.08 35:10-11

Lamlungu, October 19

Muponye maukonde anu kuti muphe nsomba.​—Luka 5:4.

Yesu anatsimikizira mtumwi Petulo kuti Yehova adzamuthandiza. Iye ataukitsidwa anathandiza Petulo ndi atumwi anzake kuphanso nsomba m’njira yodabwitsa. (Yoh. 21:4-6) Mosakayikira zimenezi zinatsimikizira Petulo kuti Yehova angamuthandize kupeza zofunika pa moyo. N’kutheka kuti mtumwiyu anakumbukira zimene Yesu ananena kuti Yehova adzathandiza aliyense amene amapitiriza ‘kuika Ufumu pamalo oyamba’. (Mat. 6:33) Zonsezi zinathandiza Petulo kuti aziona kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kwambiri kuposa usodzi. Pa tsiku la Pentekosite mu 33 C.E., iye analalikira molimba mtima ndipo anathandiza anthu ambiri kuti amve uthenga wabwino. (Mac. 2:14, 37-41) Pambuyo pake anathandiza Asamariya komanso anthu amitundu ina kuti ayambe kukhulupirira Khristu. (Mac. 8:14-17; 10:44-48) Apatu Yehova anagwiritsa ntchito kwambiri Petulo kuti athandize anthu a mitundu yonse kuti abwere mumpingo wa Chikhristu. w23.09 40:1, 11

Lolemba, October 20

Ngati simundiuza zimene ndalota n’kundimasulira, ndikudulani nthulinthuli.​—Dan. 2:5.

Patatha zaka pafupifupi ziwiri kuchokera pamene Ababulo anawononga mzinda wa Yerusalemu, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inasokonezeka maganizo ndi zimene inalota zokhudza chifaniziro chachikulu kwambiri. Mfumuyi inaopseza kuti ipha amuna onse anzeru kuphatikizapo Danieli ngati sakanaiuza zomwe inalota komanso kumasulira kwake. (Dan. 2:3-5) Danieli ankafunika kuchitapo kanthu mwamsanga chifukwa ngati sakanatero anthu ambiri akanaphedwa. Iye “anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.” (Dan. 2:16) Apatu anasonyeza kulimba mtima komanso chikhulupiriro. Palibe paliponse pamene pamasonyeza kuti Danieli anali atamasulirapo maloto. Iye anapempha anzake kuti “apemphere kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo n‘kuwaululira chinsinsi chimenechi.” (Dan. 2:18) Yehova anayankha mapemphero amenewo. Mothandizidwa ndi Mulungu, Danieli anamasulira maloto a Nebukadinezara ndipo iye ndi anzake sanaphedwe. w23.08 33:4

Lachiwiri, October 21

Amene adzapirire mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.​—Mat. 24:13.

Muziganizira ubwino wokhala woleza mtima. Tikakhala oleza mtima timakhala osangalala komanso odekha. Ndipotu kukhala ndi khalidweli kungatithandize kuti tiziganiza bwino komanso tikhale ndi thanzi labwino. Tikamachita zinthu moleza mtima ndi ena, timakhala nawo pa ubwenzi wabwino. Timakhalanso ogwirizana kwambiri mumpingo. Ngati wina watikhumudwitsa sitimakwiya msanga, zomwe zimachititsa kuti zinthu zisaipe kwambiri. (Sal. 37:8; Miy. 14:29) Koposa zonse, timakhala tikutsanzira Atate wathu wakumwamba ndipo timakhala naye pa ubwenzi wabwino kwambiri. Kunena zoona, kuleza mtima ndi khalidwe losangalatsa komanso lothandiza kwambiri. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kuleza mtima kungakhale kophweka. Koma mothandizidwa ndi Yehova, tikhoza kupitiriza kukhala ndi khalidweli. Pamene tikuyembekezera moleza mtima dziko latsopano, tisamakayikire kuti “Diso la Yehova limayang’ana anthu amene amamuopa, amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.” (Sal. 33:18) Tiyeni tonse tikhale otsimikiza mtima kuti tipitirizabe kukhala oleza mtima. w23.08 35:7, 16-17

Lachitatu, October 22

Chikhulupiriro pachokha, ngati chilibe ntchito zake, ndi chakufa.​—Yak. 2:17.

Yakobo ananena kuti munthu angamanene kuti ali ndi chikhulupiriro, koma zochita zake sizikusonyeza zimenezo. (Yak. 2:1-5, 9) Yakobo anafotokozanso za munthu yemwe anaona “m’bale kapena mlongo alibe zovala” koma sanamuthandize. Ngakhale munthu ameneyu atamanena kuti ali ndi chikhulupiriro, zingakhale zosamveka. (Yak. 2:14-16) Yakobo anatchula Rahabi monga chitsanzo cha munthu yemwe anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake. (Yak. 2:25, 26) Iye anali atamva zokhudza Yehova ndiponso kuti ndi yemwe ankathandiza Aisiraeli. (Yos. 2:9-11) Rahabi anasonyeza chikhulupiriro mwa zochita zake poteteza Aisiraeli awiri omwe anabwera kudzafufuza dziko lawo ndipo moyo wawo unali pangozi. Izi zinachititsa kuti mayi wochimwayu, yemwenso sanali Mwisiraeli, aonedwe kuti ndi wolungama ngati mmene Abulahamu analili. Chitsanzo chake chimasonyeza kufunika kokhala ndi chikhulupiriro komanso ntchito zake. w23.12 50:12-13

Lachinayi, October 23

Muzike mizu ndiponso mukhale okhazikika pamaziko.​—Aef. 3:17.

Monga Akhristu, sitimangokhutira ndi kumvetsa mfundo zoyambirira za m’Baibulo. Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, timafunitsitsanso kudziwa “ngakhale zinthu zozama za Mulungu.” (1 Akor. 2:9, 10) Bwanji osakonza zoti mufufuze mozama zinthu zomwe zingakuthandizeni kuti mukhale pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Mwachitsanzo, mungafufuze mmene anasonyezera kuti ankakonda atumiki ake akale komanso mmene zimenezo zimasonyezera kuti inunso amakukondani. Mungaphunzirenso zimene Yehova ankafuna kuti Aisiraeli azichita pomulambira n’kuziyerekezera ndi zimene amafuna kuti ifenso tizichita pomulambira masiku ano. Kapenanso mungaphunzire mozama zokhudza maulosi amene Yesu anakwaniritsa pa utumiki wake padziko lapansi. Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani lingakuthandizeni kuti muzisangalala pophunzira. Kuphunzira Baibulo mozama kungalimbitse chikhulupiriro chanu komanso kungakuthandizeni kuti ‘mumudziwedi Mulungu.’—Miy. 2:4, 5 w23.10 44:3-5

Lachisanu, October 24

Koposa zonse, muzikondana kwambiri chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.​—1 Pet. 4:8.

Mawu amene mtumwi Petulo anagwiritsa ntchito akuti “muzikondana kwambiri,” angatanthauze “kutambasula.” Mbali yachiwiri ya vesili ikufotokoza zotsatira za chikondi chimenechi. Ikuti chimakwirira machimo ochuluka a abale athu. Zili ngati timagwira chikondichi ndi manja awiri ngati mmene tingagwirire nsalu, n’kuchitambasula kuti chiphimbe, osati machimo ochepa, koma “machimo ochuluka.” Mawu akuti kuphimba, kapena kuti “kukwirira,” akufotokoza za kukhululuka. Mofanana ndi nsalu yomwe ingaphimbe malo akuda pa chovala, chikondi chimaphimba zimene abale athu amalakwitsa. Tiyenera kumakonda kwambiri abale athu moti tikhoza kuwakhululukira zolakwa zawo, ngakhale pamene kuchita zimenezi kungakhale kovuta. (Akol. 3:13) Tikakhululukira ena timasonyeza kuti timawakonda kwambiri komanso timafuna kusangalatsa Yehova. w23.11 47:13-15

Loweruka, October 25

Safani anayamba kuwerengera mfumu bukulo.​—2 Mbiri 34:18.

Atakula, Mfumu Yosiya anayamba kukonzanso kachisi. Pogwira ntchitoyi “anapeza buku la Chilamulo cha Yehova loperekedwa ndi dzanja la Mose.” Mfumuyi itamva zimene zinawerengedwa, nthawi yomweyo inasintha kuti itsatire malangizo a m’bukuli. (2 Mbiri 34:14, 19-21) Kodi mumafuna kuti muziwerenga Baibulo tsiku lililonse? Ngati mukuyesa kale kuchita zimenezi kodi zinthu zikukuyenderani bwanji? Kodi mumasunga mavesi ena ake omwe mukuona kuti angakuthandizeni? Yosiya ali ndi zaka pafupifupi 39, analakwitsa zinthu ndipo zinachititsa kuti aphedwe. Iye anadzidalira m’malo mopempha malangizo kwa Yehova. (2 Mbiri 35:20-25) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Kaya ndife wamkulu kapena wamng’ono kapenanso takhala tikuphunzira Baibulo kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenera kupitiriza kufunafuna Yehova. Zimenezi zikuphatikizapo kupempha Yehova nthawi zonse kuti atipatse malangizo, kuphunzira Mawu ake komanso kumvera malangizo a Akhristu olimba mwauzimu. Tikamachita zimenezi tidzapewa kulakwitsa kwambiri zinthu ndipo tidzakhala osangalala.—Yak. 1:25. w23.09 38:15-16

Lamlungu, October 26

Mulungu amatsutsa odzikuza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.

Baibulo limatchula zitsanzo zambiri za akazi amene ankakonda Yehova komanso kumutumikira. Iwo anali “ochita zinthu mosapitirira malire” ndiponso “okhulupirika pa zinthu zonse.” (1 Tim. 3:11) Kuwonjezera pamenepo, Akhristu achitsikana angapeze mumpingo wawo alongo olimba mwauzimu amene angamawatsanzire. Ngati ndinu mlongo wachitsikana, mungachite bwino kupeza alongo a Chikhristu olimba mwauzimu amene mungamawatsanzire. Muziona makhalidwe awo abwino. Khalidwe lofunika kwambiri kuti Mkhristu akule mwauzimu ndi kudzichepetsa. Mkazi wodzichepetsa amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso anthu ena. Mwachitsanzo, mkazi amene amakonda Yehova amakhala wodzichepetsa n’kumatsatira malangizo amene Yehova anapereka okhudza mutu wa banja ndi mutu wa mpingo.—1 Akor. 11:3. w23.12 52:3-5

Lolemba, October 27

Amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo.—Aef. 5:28.

Yehova amafuna kuti mwamuna azikonda mkazi wake ndipo azimupezera zofunika pa moyo, azikhala mnzake wapamtima komanso azimuthandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehovayo. Kuganiza bwino, kulemekeza akazi komanso kukhala odalirika, kungakuthandizeni kuti mukhale mwamuna wabwino. Mukadzakwatira, mukhoza kudzakhala ndi ana. Ndiye kodi mungaphunzire chiyani kwa Yehova pa nkhani yokhala bambo wabwino? (Aef. 6:4) Yehova ankauza Mwana wake Yesu kuti amamukonda ndiponso kuti amamusangalatsa kwambiri. (Mat. 3:17) Nanunso mukadzakhala ndi ana, muzidzawauza pafupipafupi kuti mumawakonda. Nthawi zonse muzidzawayamikira akachita zabwino. Abambo amene amatsanzira Yehova, amathandiza ana awo kuti akule mwauzimu. Mungakonzekere udindo umenewu posamalira mwachikondi anthu a m’banja lanu ndiponso a mumpingo. Komanso pouza anthu ena kuti mumawakonda ndiponso kuwayamikira.—Yoh. 15:9. w23.12 53:17-18

Lachiwiri, October 28

[Yehova] adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.​—Yes. 33:6.

Ngakhale kuti ndife atumiki okhulupirika a Yehova, mofanana ndi anthu onse, timakumana ndi mavuto komanso matenda. Nthawi zinanso timatsutsidwa kapena kuzunzidwa ndi anthu odana ndi anthu a Mulungu. Yehova samatiteteza kuti tisakumane ndi mavuto, koma amatilonjeza kuti adzatithandiza. (Yes. 41:10) Iye akatithandiza timapitirizabe kukhala osangalala, timasankha zinthu mwanzeru komanso timakhalabe okhulupirika kwa iye ngakhale pamene zili zovuta kutero. Yehova amatilonjeza kuti atipatsa “mtendere [wake]” wotchulidwa m’Baibulo. (Afil. 4:6, 7) Munthu akakhala ndi mtendere umenewu, mtima ndi maganizo ake zimakhala m’malo chifukwa choti ali pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mtenderewu ndi woti “anthu sangathe kuumvetsa” ndipo ndi wodabwitsa kuposa mmene tingaganizire. Kodi inunso mtima wanu unayamba wakhalapo m’malo mutapemphera kwa Yehova mochokera pansi pa mtima? Munamva choncho chifukwa cha “mtendere wa Mulungu.” w24.01 3:2, 4

Lachitatu, October 29

Moyo wanga utamande Yehova. Chilichonse cha mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.​—Sal. 103:1.

Kukonda Mulungu kumachititsa anthu okhulupirika kuti azitamanda dzina lake ndi mtima wonse. Mfumu Davide ankadziwa kuti kutamanda dzina la Yehova kumatanthauza kutamanda Yehovayo. Choncho tikamva dzinali timaganizira makhalidwe ake abwino komanso ntchito zake zodabwitsa. Davide ankafuna aziona kuti dzina la Atate wake ndi loyera komanso kumalitamanda. Iye ankafuna azichita zimenezo ndi “chilichonse cha mkati [mwake]” kapena kuti ndi mtima wonse. Mofanana ndi Davide, Alevi nawonso ankatsogolera potamanda Yehova. Modzichepetsa, iwo anavomereza kuti mawu awo sakanatha kufotokoza mokwanira ulemerero umene dzina loyera la Yehova liyenera kulandira. (Neh. 9:5) Mosakayikira, Yehova anasangalala ndi kudzichepetsa komanso kumutamanda kochokera pansi pamtima kumeneku. w24.02 6:6

Lachinayi, October 30

Mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.​—Afil. 3:16.

Yehova sadzakuonani kuti ndinu wolephera chifukwa simunakwaniritse cholinga chimene simukanatha kuchikwaniritsa. (2 Akor. 8:12) Muziphunzirapo kathu mukakumana ndi zolepheretsa. Muziganizira zomwe mwakwanitsa kale kuchita. Baibulo limanena kuti “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.” (Aheb. 6:10) Choncho inunso musamaiwale zomwe mwachita. Muziganizira zolinga zomwe mwazikwaniritsa kale kaya ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, kuuza ena zokhudza iye kapena kubatizidwa. Monga mmene mwakhala mukukwaniritsira zolinga zanu m’mbuyomu, mungapitirizenso kukwaniritsa cholinga chanu panopa. Mothandizidwa ndi Yehova, inunso mungathe kukwaniritsa cholinga chanu mofanana ndi woyendetsa boti yemwe amasangalala akafika kumene akupita. Koma kumbukirani kuti oyendetsa boti ambiri amasangalalanso ndi ulendo wawo. Inunso mukayesetsa kuti mukwaniritse cholinga chanu chauzimu, muzisangalala ndi mmene Yehova akukuthandizirani komanso kukudalitsirani. (2 Akor. 4:7) Ndipo ngati simungafooke mudzapeza madalitso ambiri.—Agal. 6:9. w23.05 24:16-18

Lachisanu, October 31

Atatewo amakukondani chifukwa munandikonda ndipo mwakhulupirira kuti ine ndinabwera monga nthumwi ya Mulungu.​—Yoh. 16:27.

Yehova amafunitsitsa kuuza anthu omwe amawakonda kuti amasangalala nawo. Malemba amatchula nthawi ziwiri pomwe iye anauza Yesu kuti ndi Mwana wake wokondedwa ndipo amasangalala naye. (Mat. 3:17; 17:5) Kodi mungakonde kumva Yehova akukutsimikizirani kuti amasangalala nanu? Iye salankhula nafe mwachindunji koma amatilankhula kudzera m’Mawu ake. ‘Tingamve’ mawu a Yehova onena kuti amasangalala nafe tikamawerenga mawu a Yesu m’mabuku a Uthenga Wabwino. Yesu ankatsanzira ndendende makhalidwe a Atate wake. Choncho tikamawerenga kuti Yesu ankasangalala ndi otsatira ake okhulupirika, omwe sanali angwiro, timadziwa kuti Yehova amasangalalanso ndi ifeyo. (Yoh. 15:9, 15) Tikakumana ndi mavuto sizitanthauza kuti Mulungu sakusangalala nafe. M’malomwake, zimenezi zimatipatsa mwayi wosonyeza kuti timakonda kwambiri Mulungu ndipo timamukhulupirira.—Yak. 1:12. w24.03 13:10-11

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani