Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA FEBRUARY 27, 2017–MARCH 5, 2017
1 “Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino”
Nkhaniyi ikufotokoza lemba la chaka cha 2017 lomwe likutilimbikitsa kudalira Yehova tikakumana ndi mavuto. Tiona zitsanzo zakale zotithandiza kuti tizidalira Yehova, uku tikuchita zonse zimene tingathe pothana ndi mavuto athu komanso pothandiza ena.
MLUNGU WA MARCH 6-12, 2017
2 Ufulu Wosankha Zochita Ndi Mphatso Yapadera
M’nkhaniyi, tiona zimene tingachite poyamikira mphatso ya ufulu wosankha zochita imene Mulungu anatipatsa. Tionanso zimene tingachite kuti tiziigwiritsa ntchito bwino. Nkhaniyi itithandizanso kuti tizilemekeza ufulu wa ena wosankha zochita.
MLUNGU WA MARCH 13-19, 2017
3 Kudzichepetsa N’kofunika Kwambiri
MLUNGU WA MARCH 20-26, 2017
4 Kodi Tingatani Kuti Nthawi Zonse Tizikhala Odzichepetsa?
Nkhani zimenezi zitithandiza kumvetsa bwino khalidwe la kudzichepetsa. Nkhani yoyamba ikufotokoza zimene kudzichepetsa kumatanthauza komanso zimene sikutanthauza. Nkhani yachiwiri itithandiza kudziwa zimene tingachite kuti nthawi zonse tizikhala odzichepetsa.
MLUNGU WA MARCH 27, 2017–APRIL 2, 2017
5 ‘Zinthu Zimenezo Uziziphunzitsa kwa Anthu Okhulupirika’
Abale audindo akamakula pamafunika ena achinyamata oti azigwira ntchito zimene achikulirewo ankagwira. Nkhaniyi ikufotokoza zimene abale achikulire komanso achinyamata angachite kuti zinthu ziziyenda bwino.