Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA MAY 1-7, 2017
1 Tizipereka Ulemu kwa Oyenera Kulemekezedwa
Akhristu ayenera kudziwa malire pa nkhani yopereka ulemu. Kodi ndi ndani amene tiyenera kuwapatsa ulemu, nanga n’chifukwa chiyani? M’nkhaniyi tipeza yankho la funso limeneli. Ikufotokozanso ubwino wopereka ulemu kwa anthu oyenera kulemekezedwa.
MLUNGU WA MAY 8-14, 2017
13 Muzikhulupirira Yehova Kuti Muzisankha Zochita Mwanzeru
Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kusankha zochita osati kumangokayikakayika. Koma kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kusankha zochita mwanzeru, nanga n’chiyani chingatithandize? Kodi ndi bwino kusintha zimene tinasankha? Nkhaniyi itithandiza kuyankha mafunso amenewa.
MLUNGU WA MAY 15-21, 2017
3 Tizitumikira Yehova ndi Mtima Wathunthu
MLUNGU WA MAY 22-28, 2017
4 Kodi Mumatsatira Ndi Mtima Wonse Zimene Zinalembedwa?
Popeza si ife angwiro, timalakwitsa zinthu zina. Koma kodi izi zikutanthauza kuti sitingasangalatse Yehova? M’nkhanizi tikambirana zitsanzo za mafumu 4 a ku Yuda ndipo tionanso zimene analakwitsa. Koma Yehova ankaona kuti mafumu onsewo ankamutumikira ndi mtima wathunthu. Kodi iye angaonenso kuti ifeyo timamutumikira ndi mtima wathunthu ngakhale kuti timalakwitsa zinthu zina?