Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA AUGUST 28, 2017—SEPTEMBER 3, 2017
7 Muzifunafuna Chuma Chenicheni
Nkhaniyi ikufotokoza mmene tingagwiritsire ntchito chuma chathu kuti ‘tipeze mabwenzi’ kumwamba. (Luka 16:9) Ikufotokozanso zimene zingatithandize kuti tisakhale akapolo a ndalama komanso kuti tizitumikira Yehova mwakhama.
MLUNGU WA SEPTEMBER 4-10, 2017
12 “Lirani ndi Anthu Amene Akulira”
Kodi n’chiyani chingathandize anthu amene aferedwa? Yehova amalimbikitsa anthu oterewa pogwiritsa ntchito Yesu Khristu, Malemba komanso mpingo wachikhristu. Nkhaniyi ikufotokoza zimene zingalimbikitse munthu amene waferedwa komanso mmene anthu ena angamuthandizire.
MLUNGU WA SEPTEMBER 11-17, 2017
17 N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kutamanda Yehova?
Salimo 147 limalimbikitsa anthu a Mulungu mobwerezabwereza kuti azitamanda Yehova. Kodi n’chifukwa chiyani munthu amene analemba salimoli ankafuna kuti Mulungu azitamandidwa? Nkhaniyi iyankha funsoli komanso ifotokoza chifukwa chake ifenso tiyenera kukhala ofunitsitsa kutamanda Mulungu.
MLUNGU WA SEPTEMBER 18-24, 2017
22 ‘Mulungu Akwaniritse Zofuna Zanu’
Abale ndi alongo ambiri akuchita utumiki wa nthawi zonse ali achinyamata. Kodi inunso muli ndi cholinga chimenechi? Munkhaniyi muli malangizo abwino ochokera m’Malemba omwe angakuthandizeni kudzakhala ndi tsogolo labwino.