Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA SEPTEMBER 25, 2017–OCTOBER 1, 2017
3 Kodi Mukhoza Kuyembekezera Moleza Mtima?
MLUNGU WA OCTOBER 2-8, 2017
8 ‘Mtendere wa Mulungu Umaposa Kuganiza Mozama Kulikonse’
Nkhani yoyamba ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kuyembekezera Yehova. Tionanso kuti zitsanzo za amuna ndi akazi okhulupirika akale zingatithandize kuti tizidikira moleza mtima. Nkhani yachiwiri ikusonyeza kuti Yehova akhoza kuchita zinthu zimene sitikuyembekezera. Nkhaniyi ingatithandize kumukhulupirira n’kumadikira moleza mtima kuti atithandize.
MLUNGU WA OCTOBER 9-15, 2017
17 Vulani Umunthu Wakale Ndipo Musauvalenso
MLUNGU WA OCTOBER 16-22, 2017
22 Valani Umunthu Watsopano Ndipo Musauvulenso
Nkhani yoyamba ikufotokoza tanthauzo la kuvula umunthu wakale komanso chifukwa chake tiyenera kuchita zimenezi mwamsanga. Ikufotokozanso zimene tingachite kuti tisauvalenso. Nkhani yachiwiri ikufotokoza makhalidwe angapo omwe amapanga umunthu watsopano. Ikufotokozanso mmene tingasonyezere makhalidwewa pa moyo wathu komanso mu utumiki.