Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA DECEMBER 25-31, 2017
Kuyambira kale, anthu a Yehova amaona kuti kuimba ndi kofunika kwambiri polambira Mulungu. Koma anthu ena sakonda kuimba pa gulu. Kodi tingatani kuti tisamachite mantha kuimba nyimbo zotamanda Yehova? Nkhaniyi ikufotokoza zifukwa zomveka zotichititsa kuimba mosangalala komanso zimene zingatithandize kuti tiziimba bwino.
MLUNGU WA JANUARY 1-7, 2018
8 Kodi Mumathawira kwa Yehova?
MLUNGU WA JANUARY 8-14, 2018
13 Tsanzirani Chilungamo ndi Chifundo cha Yehova
Tingaphunzire mfundo zofunika pa nkhani ya mizinda yothawirako ku Isiraeli. Munkhani yoyamba tiona zimene anthu ochimwa angachite kuti athawire kwa Yehova masiku ano. Munkhani yachiwiri tiona kuti chitsanzo cha Yehova chimatithandiza kukhululukira ena, kulemekeza moyo komanso kuchita zinthu mwachilungamo.
MLUNGU WA JANUARY 15-21, 2018
20 Pewani Kutengera Maganizo a M’dzikoli
MLUNGU WA JANUARY 22-28, 2018
25 Musalole Kuti Chilichonse Chikulepheretseni Kulandira Mphoto
Nkhani ziwirizi zili ndi malangizo amene Paulo analembera Akhristu a ku Kolose. Nkhani yoyamba ikufotokoza zimene tiyenera kuchita ngati tamva maganizo a m’dzikoli omwe tikhoza kukopeka nawo. Nkhani yachiwiri ikutikumbutsa zimene tingachite kuti tipewe zinthu zimene zingatilepheretse kudzalandira madalitso amene Yehova walonjeza.