Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA JANUARY 29, 2018–FEBRUARY 4, 2018
MLUNGU WA FEBRUARY 5-11, 2018
8 “Ndili ndi Chiyembekezo mwa Mulungu”
Kodi ndi nkhani ziti za m’Baibulo zimene zinathandiza Akhristu kukhulupirira kuti akufa adzauka? Kodi nkhanizo komanso zimene anthu ena akale ankakhulupirira pa nkhaniyi zingakuthandizeni bwanji kukhala ndi chiyembekezo? Nkhani ziwirizi zikuthandizani kukhulupirira kwambiri kuti akufa adzauka.
MLUNGU WA FEBRUARY 12-18, 2018
18 Makolo, Thandizani Ana Anu Kupeza Nzeru Kuti Adzapulumuke
MLUNGU WA FEBRUARY 19-25, 2018
23 Achinyamata, “Pitirizani Kukonza Chipulumutso Chanu”
Pa anthu masauzande ambiri amene amabatizidwa chaka chilichonse pamakhala achinyamata ambiri. Munthu akabatizidwa amadalitsidwa kwambiri koma amakhalanso ndi udindo waukulu. Ngati ndinu makolo, kodi mungathandize bwanji ana anu kuti akhale ndi cholinga choti abatizidwe? Kodi achinyamata amene anabatizidwa komanso amene akufuna kubatizidwa angalimbitse bwanji ubwenzi wawo ndi Yehova?