Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA APRIL 30, 2018–MAY 6, 2018
3 Munthu Ayenera Kubatizidwa Kuti Akhale Mkhristu
MLUNGU WA MAY 7-13, 2018
8 Makolo, Kodi Mukuthandiza Ana Anu Kuti Ayenerere Kubatizidwa?
Kodi cholinga chathu tikamaphunzitsa anthu Baibulo chiyenera kukhala chiyani? N’chifukwa chiyani si nzeru kuzengereza kubatizidwa? N’chifukwa chiyani makolo ena amalimbikitsa ana awo kuti asabatizidwe msanga? Nkhani ziwirizi ziyankha mafunso amenewa komanso ena.
MLUNGU WA MAY 14-20, 2018
14 Kuchereza Alendo Ndi Kofunika Kwambiri
Mtumwi Petulo anauza Akhristu a nthawi yake kuti: “Muzicherezana.” (1 Pet. 4:9) N’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira kwambiri malangizo amenewa masiku ano? Nanga tingawatsatire m’njira ziti? Kodi tingatani ngati taitanidwa? Mafunso amenewa ayankhidwa munkhaniyi.
MLUNGU WA MAY 21-27, 2018
23 Mulungu Amatilangiza Chifukwa Chotikonda
MLUNGU WA MAY 28, 2018–JUNE 3, 2018
28 “Mverani Malangizo Kuti Mukhale Anzeru”
Nkhanizi zikusonyeza kuti Yehova ndi Atate wathu amene amatipatsa malangizo kapena chilango chifukwa chotikonda. Koma kodi malangizo a Yehova amatithandiza bwanji? Nanga amapereka bwanji malangizo kapena chilango? Kodi ifeyo tiyenera kutani akatipatsa malangizo kapena chilango? Nanga tingatani kuti tikhale odziletsa? Nkhani ziwirizi ziyankha mafunso amenewa.