CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | TITO 1–FILIMONI
“Uike Akulu”
Paulo anauza Tito kuti ‘aike akulu mumzinda uliwonse.’ Zimenezi ndi zomwenso oyang’anira madera amachita akamaika akulu m’mipingo.
BUNGWE LOLAMULIRA
Potsatira zimene zinkachitika m’nthawi ya atumwi, Bungwe Lolamulira linapereka udindo wofunika kwambiri kwa oyang’anira madera woti aziika akulu komanso atumiki othandiza.
OYANG’ANIRA MADERA
Woyang’anira dera aliyense ayenera kuchita zinthu mosamala kwambiri komanso kupemphera asanaike munthu amene akulu amuvomereza kuti akhale paudindo.
AKULU
Ngakhale munthu ataikidwa paudindo, ayenera kupitirizabe kukwaniritsa ziyeneretso za m’Malemba.