January 27–February 2
GENESIS 9-11
Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Dziko Lonse Lapansi Linali ndi Chilankhulo Chimodzi”: (10 min.)
Gen. 11:1-4—Anthu ena anayamba kumanga mzinda ndi nsanja motsutsana ndi cholinga cha Mulungu (it-1 239; it-2 202 ¶2)
Gen. 11:6-8—Yehova anasokoneza chilankhulo chawo (it-2 202 ¶3)
Gen. 11:9—Anthuwo anasiya kumanga ndipo anabalalikira mbali zosiyanasiyana (it-2 472)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 9:20-22, 24, 25—N’chifukwa chiyani Nowa anatemberera Kanani m’malo mwa Hamu? (it-1 1023 ¶4)
Gen. 10:9, 10—Kodi Nimurodi anakhala bwanji “mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova”? (it-2 503)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 10:6-32 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo ndipo kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: N’chiyani chikusonyeza kuti ofalitsawa anali limodzi pamene amakonzekera ulendo wobwerezawu? Kodi m’bale uja anachita chiyani kuti asonyeze mwininyumba chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira n’kuyambitsa phunziro la Baibulo?
Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri. (th phunziro 4)
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza wachiwiri, kenako yambani phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa. (th phunziro 2)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Muzigwira Ntchito Yanu Mwaluso”: (15 min.) Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lvs mutu 15 ndime 1-9
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 144 ndi Pemphero