Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb21.03 25
  • Muzisankha Anzanu Mwanzeru

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzisankha Anzanu Mwanzeru
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Muzisankha Mwanzeru Anthu Ocheza Nawo
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kodi Zochita za Munthu Mmodzi Zingasinthe Zinthu?
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Anzanu Azikhala Anthu Amene Amakonda Yehova
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21.03 25
Atsikana a Chimowabu akuitana anyamata a Chiisiraeli kuti awatsatire.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisankha Anzanu Mwanzeru

Zimene zinachitikira Aisiraeli m’zigwa za Mowabu ndi chenjezo kwa Akhristufe. (1Ak 10:6, 8, 11) Aisiraeli amene anayamba kugwirizana ndi atsikana achimowabu, amene anali achiwerewere komanso ankalambira mafano, anachita machimo aakulu. Zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu. (Nu 25:9) Nafenso tili ndi anzathu akuntchito, akusukulu, oyandikana nawo nyumba, achibale komanso anthu ena odziwana nawo amene salambira Yehova. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa nkhani ya m’Baibulo imeneyi zokhudza kuopsa kogwirizana ndi anthu ngati amenewa?

ONERANI MBALI YA VIDIYO YAKUTI ZITSANZO ZOTICHENJEZA MASIKU ANO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Zitsanzo Zotichenjeza Masiku Ano.’ Zimiri akuuza Yamini komanso anthu ena zokhudza akazi a Chimowabu.

    Kodi ndi maganizo olakwika ati amene Zimiri ndi anthu ena anauza Yamini?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti ‘Zitsanzo Zotichenjeza Masiku Ano.’ Pinihasi akukambirana ndi Yamini

    Kodi Pinihasi anathandiza bwanji Yamini kuti ayambe kuona zinthu moyenera?

  • Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kukhala waubwenzi kwa munthu wosalambira Yehova ndi kukhala bwenzi la munthuyo?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala posankha anzathu apamtima ngakhale mumpingo?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa magulu a pa intaneti ochezera a anthu amene sitiwadziwa?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani