Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • w24.05 101
  • Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Nkhani Yofanana
  • Ndine Msilikali wa Khristu
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Yehova Amatithandiza Kuti Zinthu Zizitiyendera Bwino
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Kapolo Amene Ankamvera Mulungu
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Ankasamalira Banja Lake Komanso Anakhalabe Wokhulupirika
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
w24.05 101

ZOTI NDIPHUNZIRE

Kupirira Zinthu Zopanda Chilungamo

Werengani Genesis 37:23-28; 39:17-23 kuti muone zinthu zopanda chilungamo zimene Yosefe anapirira.

Ganizirani nkhani yonse. N’chifukwa chiyani Yosefe anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo? (Gen. 37:3-11; 39:1, 6-10) Kodi Yosefe anapirira kwa nthawi yaitali bwanji? (Gen. 37:2; 41:46) Kodi pa nthawiyo ndi zinthu ziti zimene Yehova anamuchitira Yosefe, nanga ndi zinthu ziti zimene sanamuchitire?​—Gen. 39:2, 21; w23.01 17 ¶13.

Fufuzani mozama. Baibulo silifotokoza ngati Yosefe anali ndi mwayi wofotokoza mbali yake pa zinthu zabodza zimene mkazi wa Potifara ankamuneneza. Kodi malemba otsatirawa angatithandize bwanji kudziwa chifukwa chimene mwina chinachititsa kuti Yosefe asayankhepo? Nanga angatithandize bwanji kudziwa chifukwa chake sitiyenera kuyembekezera kuti mfundo zonse zifotokozedwe? (Miy. 20:2; Yoh. 21:25; Mac. 21:37) Kodi ndi makhalidwe ati amene anathandiza Yosefe kuti apirire zinthu zopanda chilungamo?​—Mika 7:7; Luka 14:11; Yak. 1:2, 3.

Onani zimene mukuphunzirapo. Dzifunseni kuti:

  • ‘Kodi ndingachitiridwe zinthu zopanda chilungamo ziti chifukwa chokhala wotsatira wa Yesu?’ (Luka 21:12, 16, 17; Aheb. 10:33, 34.)

  • ‘Kodi ndingakonzekere bwanji kuti ndidzapirire zinthu zopanda chilungamo?’ (Sal. 62:7, 8; 105:17-19; w19.07 2-7.)

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani