NYIMBO 7
Yehova Ndiye Mphamvu Zathu
1. Yehova inu ndi mphamvu yathu,
Inu ndinu Mpulumutsi wathu.
Ndife Mboni za uthenga wanu,
Ngakhale anthu azitinyoza.
(KOLASI)
Yehova, thanthwe ndi mphamvu zathu,
Tilengezabe dzina lanu.
Yehova inu wamphamvuyonse,
Pobisala pathu nsanja yathu.
2. Kuwala kwanu n’kosangalatsa;
Maso athu aona cho’nadi.
Malamulo anu tawadziwa,
Tidzasankhatu Ufumu wanu.
(KOLASI)
Yehova, thanthwe ndi mphamvu zathu,
Tilengezabe dzina lanu.
Yehova inu wamphamvuyonse,
Pobisala pathu nsanja yathu.
3. Chifuniro chanu tichitabe.
Ngakhale Satana ’matinyoza.
Kaya atiphe tithandizeni
Kukhala kumbali yanu M’lungu.
(KOLASI)
Yehova, thanthwe ndi mphamvu zathu,
Tilengezabe dzina lanu.
Yehova inu wamphamvuyonse,
Pobisala pathu nsanja yathu.
(Onaninso 2 Sam. 22:3; Sal. 18:2; Yes. 43:12.)