NYIMBO 9
Yehova Ndi Mfumu Yathu
1. Kondwa lemekeza Yehova,
Kumwamba kulengeza chilungamo.
Mosangalala tiimbire Mulungu,
Tiuze onse ntchito zake.
(KOLASI)
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu.
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu.
2. Nena za kukwezeka kwake,
Chifukwa ndiye wotipulumutsa.
Yehova, tiyenera kumutamanda.
Tiyenitu timugwadire.
(KOLASI)
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu.
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu.
3. Wakhazikitsatu Ufumu.
Waika Mwana wake pampandowo.
Milungu yabodza
ichite manyazi,
Titamande Yehova yekha.
(KOLASI)
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu.
Kumwamba kukondwe, Dziko likondwere,
Chifukwa Yehova ndi Mfumu.
(Onaninso 1 Mbiri 16:9; Sal. 68:20; 97:6, 7.)