NYIMBO 20
Munapereka Mwana Wanu Wobadwa Yekha
zosindikizidwa
1. Yehova, tinali
opanda tsogolo.
Komano dipo
lathandiza tonse.
Tikudzipereka,
kwa inu kosatha.
Tiphunzitse ena,
Akudziweninso.
(KOLASI)
Mwana wanu yekha,
munamupereka.
Tidzakuimbirani,
za mphatsoyi kwamuyaya.
2. Chifundo chanucho
ndi chachikuludi.
Komanso timakonda
dzina lanu.
Yoposa zonsezi,
ndi mphatso ya Yesu.
Anatifera kuti
tipulumuke.
(KOLASI)
Mwana wanu yekha,
munamupereka.
Tidzakuimbirani,
za mphatsoyi kwamuyaya.
(KUMALIZA)
Yehova, Atate, tikuthokozatu.
Mphatsoyi munatipatsadi kwamuyaya.
(Onaninso Yoh. 3:16; 15:13.)