NYIMBO 60
Akamvera Adzapeza Moyo
zosindikizidwa
1. Mulungu akufuna
tichenjeze anthu
Kuti tsiku la mkwiyo
wake likubwera.
(KOLASI)
Akamvera adzapeza,
Inde moyo wosatha.
Nafe tidzapulumuka,
Tikafalitsa uthenga,
Uthenga.
2. Tili ndi uthenga
woti tiuze anthu.
Tiitane anthu abwere
kwa Mulungu.
(KOLASI)
Akamvera adzapeza,
Inde moyo wosatha.
Nafe tidzapulumuka,
Tikafalitsa uthenga,
Uthenga.
(VESI LOKOMETSERA)
Mwamsanga tilengeze,
Anthu amve, aphunzire.
Cho’nadi tiphunzitse,
Kuti moyo adzapeze.
(KOLASI)
Akamvera adzapeza,
Inde moyo wosatha.
Nafe tidzapulumuka,
Tikafalitsa uthenga,
Uthenga.
(Onaninso 2 Mbiri 36:15; Yes. 61:2; Ezek. 33:6; 2 Ates. 1:8.)