NYIMBO 134
Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu
zosindikizidwa
1. Mwamuna ’kakhala bambo
Mkazinso akakhala ndi mwana,
Ayenera kukumbukira,
Mwanayo si wawo okha.
Ndi mphatso yochoka kwa M’lungu;
Amapatsa chikondi ndi moyo.
Amapereka malangizo
Othandizadi kwa makolo.
(KOLASI)
Mphatsoyi ndi yopatulika;
Ndipo muisamalire.
M’phunzitseni mwana cho’nadi;
Ndipo mudzamuthandiza.
2. Mawu onse a Mulungu—
Azikhalatu pamtima panu.
Muziuzanso ana anu,
Uwu ndi udindo wanu.
Muziwaphunzitsa poyenda,
Podzuka ndi pa nthawi yopuma.
Akamakula saiwala,
Adzalandira madalitso.
(KOLASI)
Mphatsoyi ndi yopatulika;
Ndipo muisamalire.
M’phunzitseni mwana cho’nadi;
Ndipo mudzamuthandiza.
(Onaninso Deut. 6:6, 7; Aef. 6:4; 1 Tim. 4:16.)