NYIMBO 71
Ndife Gulu Lankhondo la Yehova
zosindikizidwa
1. Ndife gulu lankhondo,
La M’lungu wathu.
Lotsogoleredwa ndi
Mwana wake Yesu.
Satana angatsutse,
Tilalikabe.
Ndife osaopa
Olimba mtima.
(KOLASI)
Ndife gulu lankhondo.
Tikulengeza:
“Ufumu wayamba
Kulamulira.”
2. Ndife anthu a M’lungu,
Ofunafuna,
Anthu omwe ndi nkhosa,
Zosowa za M’lungu.
Tifuna kuwapeza,
N’kuwaphunzitsa,
N’kuwalimbikitsa:
“Tizisonkhana.”
(KOLASI)
Ndife gulu lankhondo.
Tikulengeza:
“Ufumu wayamba
Kulamulira.”
3. Ndife gulu lankhondo,
Lomvera Yesu,
Lokonzekera nkhondo,
Lolimbatu mtima.
Koma tikhale tcheru,
Kuti tisagwe.
Zinthu zikavuta,
Tisafooke.
(KOLASI)
Ndife gulu lankhondo.
Tikulengeza:
“Ufumu wayamba
Kulamulira.”
(Onaninso Aef. 6:11, 14; Afil. 1:7; Filim. 2.)