NYIMBO 147
Mulungu Watilonjeza Moyo Wosatha
zosindikizidwa
1. Mulungu watilonjeza.
Moyo womwe sudzatha.
‘Ofatsa ’dzasangalala.’
Zidzachitikadi.
(KOLASI)
Tidzakhala ndithu,
Ndi moyo wosatha.
M’lungu walonjeza.
Zidzachitika.
2. Paradaiso akubwera;
Anthu adzamasuka.
Kudzakhaladi mtendere,
Wochoka kwa M’lungu.
(KOLASI)
Tidzakhala ndithu,
Ndi moyo wosatha.
M’lungu walonjeza.
Zidzachitika.
3. Akufawo adzauka,
Chisoninso chidzatha.
Mulungu adzapukuta,
Misozi ya anthu.
(KOLASI)
Tidzakhala ndithu,
Ndi moyo wosatha.
M’lungu walonjeza.
Zidzachitika.
(Onaninso Yes. 25:8; Luka 23:43; Yoh. 11:25; Chiv. 21:4.)