NYIMBO 148
Yehova Amapereka Populumukira
1. Yehova ndinudi Mulungu wamoyo;
M’chilengedwe chonse
Mphamvu zaoneka.
Palibe M’lungu wina angachite
—zimene
Inu mumachita.
(KOLASI)
Yehova ndiye pothawira pathu.
Tidzaonadi kuti iye ndi Thanthwe.
Tilengeze molimba mtima
mphamvu zake.
Yehova m’pothawira pathu,
tim’tamande.
2. Zingwe za imfa zingandizungulire,
ndidalira inu,
“Mundipatse mphamvu,
mundilimbitse mtima.”
Mumve kulira kwanga
“Ndibiseni M’lungu.”
(KOLASI)
Yehova ndiye pothawira pathu.
Tidzaonadi kuti iye ndi Thanthwe.
Tilengeze molimba mtima
mphamvu zake.
Yehova m’pothawira pathu,
tim’tamande.
3. Mudzagunda ngati
mabingu kumwamba.
Adzanjenjemera;
Adani anuwo.
Mudzakhala chimene mukufuna
kukhala
Onse adzaona.
(KOLASI)
Yehova ndiye pothawira pathu.
Tidzaonadi kuti iye ndi Thanthwe.
Tilengeze molimba mtima
mphamvu zake.
Yehova m’pothawira pathu,
tim’tamande.
(Onaninso Sal. 18:1, 2; 144:1, 2.)