PHUNZIRO 20
Mawu Omaliza Abwino
Mlaliki 12:13, 14
MFUNDO YAIKULU: Mawu anu omaliza azithandiza anthu kuvomereza zimene aphunzira n’kuyamba kuzigwiritsa ntchito.
MMENE MUNGACHITIRE:
Mawu omaliza azikhala ogwirizana ndi mutu wa nkhani yonse. Muzibwereza mfundo zikuluzikulu komanso mutu wa nkhani.
Limbikitsani anthu kutsatira zimene aphunzira. Auzeni anthu zoyenera kuchita komanso zifukwa zochitira zinthuzo. Mawu anu omaliza azikhala ochokera mumtima ndipo muziwanena motsimikiza.
Mawu omaliza azikhala achidule komanso osavuta. Musatchule mfundo ina yatsopano. Mawu ake angokhala ochepa koma othandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita.