Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lff 16
  • Kubwereza Gawo 1

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza Gawo 1
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Nkhani Yofanana
  • Kubwereza Gawo 2
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kubwereza Gawo 3
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kubwereza Gawo 4
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Gawo 1
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff 16

Gawo 1 Kubwereza

zosindikizidwa

Kambiranani mafunsowa ndi mphunzitsi wanu:

Mnyamata akuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova.
  1. N’chiyani chimakusangalatsani mukaganizira zimene Baibulo limalonjeza zokhudza m’tsogolo?

    (Onani Phunziro 02.)

  2. N’chifukwa chiyani mumakhulupirira kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu?

    (Onani Phunziro 03 ndi 05.)

  3. N’chifukwa chiyani kugwiritsa ntchito dzina la Yehova n’kofunika?

    (Onani Phunziro 04.)

  4. Baibulo limanena kuti Mulungu ndi “kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Kodi mumakhulupirira zimenezi?

    (Onani Phunziro 06.)

  5. Werengani Miyambo 3:32.

    • N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi Mnzathu wabwino kwambiri amene tingakhale naye?

    • Kodi Yehova amafuna kuti anzake azichita chiyani? Kodi mumaona kuti zimene Yehova amafunazi n’zotheka kuzichita?

      (Onani Phunziro 07 ndi 08.)

  6. Werengani Salimo 62:8.

    • Kodi ndi zinthu ziti zimene munamuuzapo Yehova popemphera? Nanga ndi zinthu zinanso ziti zimene mungazipempherere?

    • Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero?

      (Onani Phunziro 09.)

  7. Werengani Aheberi 10:​24, 25.

    • Kodi misonkhano ya Mboni za Yehova ingakuthandizeni bwanji?

    • Kodi mukuona kuti mukuyeneradi kuchita khama kuti muzipezeka pamisonkhano?

      (Onani Phunziro 10.)

  8. N’chifukwa chiyani muyenera kumawerenga Baibulo tsiku lililonse? Ndi nthawi iti imene mumakonda kuwerenga Baibulo tsiku lililonse?

    (Onani Phunziro 11.)

  9. Pofika pano, ndi zinthu ziti zimene zakusangalatsani kwambiri pophunzira Baibulo?

  10. Kuchokera pamene munayamba kuphunzira Baibulo, kodi mwakumana ndi mavuto aliwonse amene akanakulepheretsani kupitiriza? N’chiyani chimene chingakuthandizeni kuti musasiye kuphunziraku?

    (Onani Phunziro 12.)

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani