Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • lff 55
  • Kubwereza Gawo 3

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza Gawo 3
  • Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Nkhani Yofanana
  • Kubwereza Gawo 2
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kubwereza Gawo 4
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Kubwereza Gawo 1
    Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
  • Muzigwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzira ndi Anthu
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
Onani Zambiri
Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale—Kuphunzira Baibulo Mokambirana
lff 55

KUBWEREZA GAWO 3

zosindikizidwa

Kambiranani mafunsowa ndi mphunzitsi wanu:

Munthu akubatizidwa.
  1. Werengani Miyambo 27:11.

    • N’chifukwa chiyani mukufuna kukhala okhulupirika kwa Yehova?

      (Onani Phunziro 34.)

  2. Kodi mungasankhe bwanji zinthu mwanzeru pa nkhani zimene Baibulo silipereka malamulo achindunji?

    (Onani Phunziro 35.)

  3. Mungatani kuti muzichita zinthu zonse moona mtima?

    (Onani Phunziro 36.)

  4. Werengani Mateyu 6:33.

    • Mungatani kuti ntchito ndi ndalama zisakulepheretseni “kufunafuna Ufumu choyamba”?

      (Onani Phunziro 37.)

  5. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumaona moyo kukhala wamtengo wapatali ngati mmene Yehova amauonera?

    (Onani Phunziro 38.)

  6. Werengani Machitidwe 15:29.

    • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumamvera lamulo la Yehova lokhudza magazi?

    • Kodi mukuona kuti zimene Mulungu amanena zokhudza magazi ndi zomveka?

      (Onani Phunziro 39.)

  7. Werengani 2 Akorinto 7:1.

    • Kodi kukhala oyera mwakuthupi komanso mwamakhalidwe kumatanthauza chiyani?

      (Onani Phunziro 40.)

  8. Werengani 1 Akorinto 6:9, 10.

    • Kodi Baibulo limapereka malangizo otani okhudza kugonana? Kodi mukuona kuti malangizo amenewa ndi omveka?

    • Kodi Baibulo limapereka malangizo otani pa nkhani ya mowa?

      (Onani Phunziro 41 ndi 43.)

  9. Werengani Mateyu 19:4-6, 9.

    • Kodi Mulungu anapereka mfundo zotani zokhudza ukwati?

    • N’chifukwa chiyani anthu ayenera kukalembetsa ku boma akamamangitsa kapena kuthetsa ukwati?

      (Onani Phunziro 42.)

  10. Kodi ndi zikondwerero komanso maholide ati amene sasangalatsa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani?

    (Onani Phunziro 44.)

  11. Werengani Yohane 17:16 ndi Machitidwe 5:29.

    • Kodi mungatani kuti musakhale mbali ya dziko?

    • Kodi mungatani ngati lamulo la anthu likutsutsana ndi lamulo la Mulungu?

      (Onani Phunziro 45.)

  12. Werengani Maliko 12:30.

    • Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumakonda Yehova?

      (Onani Phunziro 46 ndi 47.)

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani