CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | OBADIYA 1–YONA 4
Muziphunzirapo Kanthu pa Zimene Munalakwitsa
Nkhani ya Yona imasonyeza kuti Yehova satisiya tikalakwitsa zinazake. M’malomwake, amafuna kuti tiphunzirepo kanthu pa zimene talakwitsazo n’kusintha.
Kodi Yona anatani Yehova atamupatsa ntchito yoti agwire?
Kodi Yona anapempha chiyani ndipo Yehova anayankha bwanji pemphero lakelo?
Kodi Yona anasonyeza bwanji kuti anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsa?