MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zimene Tikuphunzira Kuchokera m’Buku la Yona
Yehova anachititsa kuti nkhani zosiyanasiyana za amuna ndi akazi okhulupirika zilembedwe m’Mawu ake n’cholinga choti tiphunzirepo kanthu. (Aroma 15:4) Kodi mwaphunzira zotani m’buku la Yona? Onerani vidiyo yakuti Kulambira kwa Pabanja: Yona Anaphunzira Kuti Mulungu Ndi Wachifundo, kenako yankhani mafunso otsatirawa:
Kodi ofalitsa atatu a m’vidiyoyi anakumana ndi mavuto otani?
Kodi mfundo za m’buku la Yona zingatithandize bwanji tikapatsidwa uphungu kapena tikauzidwa kuti tisiye kuchita utumiki winawake? (1 Sam. 16:7; Yona 3:1, 2)
Kodi nkhani ya Yona ingatithandize bwanji kuti tiziwaona moyenerera anthu a m’gawo lathu? (Yona 4:11; Mat. 5:7)
Kodi zimene zinachitikira Yona zingatithandize bwanji ngati tikudwala matenda aakulu? (Yona 2:1, 2, 7, 9)
Kodi mwaphunzira zotani m’vidiyoyi zomwe zikusonyeza kuti kuwerenga Baibulo komanso kuganizira zimene tawerengazo n’kofunika kwambiri?