MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Munthu Aliyense wa M’gawo Lanu
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Zekariya analosera kuti anthu a zilankhulo komanso mitundu yosiyanasiyana adzamvetsera uthenga wabwino. (Zek. 8:23) Koma kodi adzawaphunzitse anthuwa ndi ndani? (Aroma 10:13-15) Ifeyo ndi amene tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino kwa munthu aliyense wa m’gawo lathu.—od 84 ¶10-11.
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
Tizikonzekera. Kodi tikamalalikira m’gawo lathu timakumana ndi anthu a zinenero zina? Ngati ndi choncho tingathe kugwiritsa ntchito pulogalamu ya JW Language kuti tiphunzire mmene tingalalikirire mwachidule anthuwo m’zinenero zawo. Tikhozanso kugwiritsa ntchito foni kapena tabuleti yathu kuwasonyeza mmene angapezere mabuku ndi zinthu zina pa jw.org
Tizikhala tcheru. Tizilalikira anthu amene tingakumane nawo mumsewu tikamachoka kunyumba ina kupita kunyumba ina komanso anthu amene ali m’magalimoto omwe angoima. Ngati tikulalikira m’malo opezeka anthu ambiri, maganizo athu onse azikhala pa ntchito yolalikirayo
Tizichita khama. Ngati sitinapeze anthu pakhomo linalake, tizibwererakonso. Tikhoza kusintha nthawi kapena tsiku loti tipiteko n’cholinga choti tikawapeze. Anthu ena omwe sakupezekabe pakhomo, tikhoza kuwalembera kalata, kuwaimbira foni, kapenanso tingathe kungochita ulaliki wa mumsewu
Tizibwererako mwachangu. Ngati munthu wasonyeza chidwi tizibwererako mofulumira. Ngati munthuyo amalankhula chinenero china, tizifufuza munthu woyenerera woti aziphunzira naye m’chinenero chakecho. Sitiyenera kusiya kupitako kufikira atayamba kuphunzira ndi ofalitsa amene amayankhula chinenero chake.—od 94 ¶39-40
ONERANI VIDIYO YAKUTI KULALIKIRA MPAKA “KUMALEKEZERO A DZIKO LAPANSI” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi abale ndi alongo a m’vidiyoyi anakonzekera bwanji popita kukalalikira kugawo lakutali (1 Akor. 9:22, 23)
Kodi anakumana ndi mavuto otani?
Kodi anapeza madalitso otani?
Kodi ndi zinthu ziti zimene tikufuna kuchita kuti tizilalikira anthu ambiri m’gawo lathu?