MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Tizichita Zinthu Mogwirizana Tikamalalikira M’gawo la Zinenero Zambiri
Anthu amachita chidwi ndi uthenga wabwino wa Ufumu akamaumva m’chinenero chawo. N’chifukwa chake pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Yehova anakonza zoti “Ayuda ena, ochokera mu mtundu uliwonse mwa mitundu ya pansi pa thambo” amve uthenga wabwino mu “chinenero chimene anabadwa nacho.” Anachita izi ngakhale kuti anthuwo ayenera ankalankhula zinenero zomwe anthu ambiri ankadziwa pa nthawiyo monga Chiheberi kapena Chigiriki. (Mac. 2:5, 8) Masiku anonso, m’madera ena omwe anthu amalankhula zinenero zosiyanasiyana, mumakhalanso mipingo ya zinenero zosiyanasiyana ndipo mipingoyi imalalikira m’gawo limodzi. Kodi ofalitsa a m’mipingo ngati imeneyi angatani kuti azilalikira anthu onse m’gawo lawo popanda kutopetsa eni nyumba?
Muzikambirana (Miy. 15:22): Oyang’anira utumiki a mipingoyo ayenera kukumana n’kugwirizana zomwe angachite kuti azilalikira uthenga wabwino mwadongosolo. Ngati gawo lili laling’ono, mipingo ya zinenero zina ingafune kuti musamalalikire nyumba za anthu achinenero chawo. Komabe nthawi zina mipingo ya zinenero zina ingalephere kulalikira anthu a m’madera akutali ndipo ingakonde kuti mipingo ya zinenero zina imene imalalikira m’deralo isamadumphe nyumba zina ikamalalikira komanso kuti aziwauza ngati apeza anthu achidwi. (od 93 ¶37) Kapena mpingo wina ungakupempheni kuti muziwapatsa mayina komanso maadiresi a anthu omwe amalankhula chinenero chawo. (km 7/12 5, bokosi) Dziwani kuti nthawi zina khomo limodzi lingathe kukhala ndi anthu olankhula zinenero zingapo. Dongosolo limene mungakonze liyenera kugwirizana ndi zimene malamulo a m’dziko lanulo amanena pa nkhani yosunga chinsinsi cha anthu ena.
Muzichita zinthu mogwirizana (Aef. 4:16): Muzitsatira mosamala malangizo aliwonse omwe woyang’anira utumiki wakupatsani. Kodi mumaphunzira Baibulo ndi munthu yemwe chinenero chake ndi chosiyana ndi cha mpingo wanu? Wophunzirayo angapite patsogolo msanga ngati mutamupereka kumpingo kapena kagulu ka chinenero chake.
Muzikonzekera (Miy. 15:28; 16:1): Ngati mwapeza munthu wachinenero china m’gawo lanu, muziyesetsa kuti mumuuze uthenga wabwino. Musanalowe muutumiki mungachite bwino kukonzekera poganizira zinenero zimene zimapezeka m’gawo lanu komanso kupangiratu dawunilodi mabuku ndi mavidiyo a zinenerozo. Mungagwiritsenso ntchito pulogalamu ya JW Language pophunzira moni wa zinenerozo.