Ngakhale kuti zomwe zinkachitika pa mwambo wa Pasika sizinkaimira zimene zimachitika pa Chikumbutso, zimene zinkachitika pamwambowu zingatithandize kumvetsa mfundo zina. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anatchula Yesu kuti “nsembe yathu ya pasika.” (1 Akor. 5:7) Mofanana ndi mmene magazi a nkhosa omwe Aisiraeli anapaka pamafelemu a nyumba zawo anapulumutsira miyoyo ya anthu, nawonso magazi a Yesu amapulumutsa miyoyo. (Eks. 12:12, 13) Komanso pa pasika, palibe fupa la mwana wa nkhosa limene linkaphwanyidwa. Mofanana ndi zimenezi, Yesu sanathyoledwe fupa ngakhale limodzi pamene anapachikidwa, ngakhale kuti unali mwambo womwe anthu ankatsatira akamapha anthu mwa njira imeneyi.—Eks. 12:46; Yoh. 19:31-33, 36.