CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MALIKO 5-6
Yesu Ali ndi Mphamvu Zoukitsa Anthu Amene Anamwalira
Tikamalira chifukwa cha imfa ya munthu amene timam’konda, sizisonyeza kuti sitikhulupirira zoti akufa adzauka (Gen. 23:2)
Kuganizira nkhani za m’Baibulo zokhudza anthu amene anaukitsidwa kungatithandize kuti tisamakayikire zoti akufa adzauka
Kodi inuyo mumafuna mutadzaonananso ndi ndani, akufa akamadzaukitsidwa?
Kodi mumamva bwanji mukamaganizira zodzakumananso ndi anthu amenewo?