MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzitsatira Mapazi a Khristu Mosamala Kwambiri
Yesu anatipatsa chitsanzo choti tizitsatira makamaka tikamakumana ndi mayesero kapena tikamazunzidwa. (1 Pet. 2:21-23) Iye sanabwezere anthu amene ankamunyoza ndipo sanachite zimenezi ngakhale pa nthawi imene ankamva ululu. (Maliko 15:29-32) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Iye anali wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Yehova. (Yoh. 6:38) Yesu ankaganiziranso kwambiri za “chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake.”—Aheb. 12:2.
Kodi ifeyo timatani ngati anthu ena akutizunza chifukwa cha zimene timakhulupirira? Akhristu oona ‘sabwezera choipa pa choipa.’ (Aroma 12:14, 17) Tikamatsanzira Yesu n’kumapirira, tingakhalebe osangalala podziwa kuti Yehova akukondwera nafe.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:12-14.
ONERANI VIDIYO YAKUTI DZINA LA YEHOVA NDI LOFUNIKA KWAMBIRI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi Mlongo Pötzingera anagwiritsa ntchito bwanji nthawi yake mwanzeru pamene anamutsekera m’selo yayekha?
Kodi M’bale ndi Mlongo Pötzinger anakumana ndi mavuto otani pamene anali m’ndende zosiyanasiyana?
Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti apirire?
Muzitsatira mapazi a Khristu mosamala kwambiri mukamazunzidwa
a Dzinali limalembedwanso kuti Poetzinger.