CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 17-18
Muzisonyeza Kuyamikira
Kodi nkhani imeneyi ikutiphunzitsa chiyani pa nkhani yosonyeza kuyamikira?
Tisamangothokoza chamumtima koma tizichita zinthu zosonyeza kuti tikuyamikira
Munthu akamayamikira kuchokera pansi pa mtima amasonyeza kuti ali ndi makhalidwe abwino komanso amakonda Akhristu anzake
Anthu amene amafuna kusangalatsa Khristu amayesetsa kukonda komanso kuyamikira anthu onse, mosasamala kanthu kuti ndi osiyana nawo mtundu kapena chipembedzo