Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb18.08 3
  • Kumbukirani Mkazi wa Loti

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kumbukirani Mkazi wa Loti
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
  • Nkhani Yofanana
  • Kumbukirani Mkazi wa Loti
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Tizithandiza Anthu Amene Ali ndi Nkhawa
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2018
mwb18.08 3
Mkazi wa Loti anayang’ana ku Sodomu ndipo anasanduka chulu cha mchere

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kumbukirani Mkazi wa Loti

Kodi n’chifukwa chiyani mkazi wa Loti anayang’ana kumbuyo pamene ankathawa ku Sodomu? Baibulo silifotokoza chifukwa chake. (Gen. 19:17, 26) Koma tikaona nkhani yochenjeza imene Yesu ananena, n’kutheka kuti ankaganizira kwambiri zinthu zimene anasiya. (Luka 17:31, 32) Kodi tingatani kuti tipewe zimene mkazi wa Loti anakumana nazo? Sitiyenera kulola kuti kufunafuna chuma kutilepheretse kuchita zinthu zofunika kwambiri. (Mat. 6:33) Yesu ananena kuti “simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.” (Mat. 6:24) Koma bwanji ngati tikuona kuti kufunafuna chuma kwayamba kutilepheretsa kuchita zinthu zokhudza kulambira? Tiyenera kupempha kuti Yehova atithandize kuona zimene tifunika kusintha komanso kuti atipatse mphamvu yochitira zimenezi.

GANIZIRANI MFUNDO ZA M’VIDIYO YA MBALI ZITATU YAKUTI KUMBUKIRANI MKAZI WA LOTI, NDIPO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Anna ali kuntchito; Gloria ali ndi ankolo ake; Brian ndi Gloria akupemphera

    Kodi zochita zanga zingasonyeze bwanji kuti ‘ndimakumbukira mkazi wa Loti’?

    Kodi zimene Gloria ankauzidwa ndi mayi ake zinakhudza bwanji maganizo, zolankhula komanso zochita zake?

  • Kodi nkhani ya mkazi wa Loti ikutipatsa chenjezo lotani?

  • Kodi kutsatira mfundo za m’Baibulo kunathandiza bwanji Joe ndi banja lake?

  • Kodi kucheza ndi anthu olakwika kuntchito kunamusokoneza bwanji Anna?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zinthu molimba mtima anthu ena akamatikakamiza kuti tizifunafuna chuma?

  • Kodi Gloria ndi Brian anachita chiyani kuti ayambirenso kuona kuti zinthu zokhudza kulambira n’zofunika kwambiri?

  • Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zimene zasonyezedwa m’vidiyoyi?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani