CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | LUKA 19-20
Zomwe Tikuphunzira M’fanizo la Ndalama 10 za Mina
Kodi zinthu zosiyanasiyana zotchulidwa m’fanizoli zikuimira chiyani?
Mbuye akuimira Yesu
Akapolo akuimira Akhristu odzozedwa
Ndalama zimene mbuye anapatsa akapolo ake zikuimira mwayi wapadera wothandiza ena kuti akhale ophunzira a Yesu
M’fanizoli, Yesu anachenjeza Akhristu odzozedwa za zimene zingachitike ngati atayamba kukhala ndi mtima wangati wa kapolo woipa. Yesu amayembekezera kuti otsatira ake azigwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso zinthu zawo pogwira ntchito yophunzitsa anthu.
Kodi ndingatsanzire bwanji Akhristu odzozedwa pogwira ntchito yophunzitsa anthu?