CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MACHITIDWE 4-5
Anapitiriza Kulankhula Mawu a Mulungu Molimba Mtima
Kodi n’chiyani chinathandiza kuti atumwi akhale oyenerera kukhala aphunzitsi? Nanga n’chiyani chinawathandiza kuti azilankhula molimba mtima? Iwo “anali kuyenda ndi Yesu,” yemwe anali Mphunzitsi Wamkulu ndipo anaphunzira kuchokera kwa iye. (Mac. 4:13) Kodi ndi zinthu ziti zimene tikuphunzira kwa Yesu zomwe zingatithandize kuti tikhale aphunzitsi aluso?