Akulandira munthu amene wabwera kumwambo wa Chikumbutso
Zimene Tinganene
●○○ ULENDO WOYAMBA
Funso: Kodi Yesu anali ndani?
Lemba: Mat. 16:16
Funso la Ulendo Wotsatira: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
○●○ ULENDO WOBWEREZA WOYAMBA
Funso: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?
Lemba: Mat. 20:28
Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe ya dipo ya Yesu?
○○● ULENDO WOBWEREZA WACHIWIRI
Funso: Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe ya dipo ya Yesu?
Lemba: Yoh. 17:3
Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova kumachitika zotani?
NTCHITO YOGAWIRA KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO (March 23–April 19):
Tikukuitanani kumwambo wofunika kwambiri. Kapepala kanu ndi kameneka. Lachisanu pa 19 April, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse adzasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani ya mutu wakuti, “Yesetsani Kuti Mudzapeze Moyo Weniweni” yomwe idzakambidwe kutatsala mlungu umodzi kuti mwambowu uchitike.
Funso la Ulendo Wotsatira Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?