MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Ntchito Zabwino Zimene Yehova Sangaziiwale
Atumiki a Yehova onse akhoza kuchita zinthu zomwe Yehova sangaziiwale. Monga mmene kholo limachitira mwana wake akachita zinthu zabwino, Yehova sangaiwale zimene timachita komanso chikondi chimene timasonyeza pa dzina lake. (Mat. 6:20; Aheb. 6:10) N’zoona kuti luso ndi zochitika pa moyo wathu zingakhale zosiyana. Komabe, ngati titachita zonse zomwe tingathe potumikira Yehova, tikhoza kumakhala osangalala. (Agal. 6:4; Akol. 3:23) Kwa zaka zambiri, abale ndi alongo ambirimbiri akhala akutumikira pa Beteli. Kodi nanunso mungakonde kutumikira pa Beteli? Ngati n’zosatheka, kodi pali wina amene mungamulimbikitse kuti ayambe utumikiwu? Kapena mungathandize m’bale kapena mlongo wina amene akuchita utumikiwu kuti apitirizebe?
ONERANI VIDIYO YAKUTI, KODI MUNGAKONDE KUTUMIKIRA PA BETELI? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi cholinga chanu chiyenera kukhala chotani ngati mukufuna kukatumikira pa Beteli?
Kodi ndi madalitso ati omwe ena apeza chifukwa chotumikira pa Beteli?
Kodi ndi zinthu ziti zomwe munthu ayenera kukwaniritsa kuti ayambe utumiki wa pa Beteli?
Kodi mungafunsire bwanji utumiki wa pa Beteli?