Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb19.11 8
  • Yehova Amadziwa Zimene Timafunikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova Amadziwa Zimene Timafunikira
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
  • Nkhani Yofanana
  • Misonkhano Yachigawo Imatipatsa Mwayi Wosonyezana Chikondi
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2019
mwb19.11 8
Alongo akuomba m’manja pamsonkhano wachigawo

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yehova Amadziwa Zimene Timafunikira

Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa chakudya “pa nthawi yoyenera.” Zimenezi ndi umboni wakuti Yehova amene akutsogolera kapoloyu amadziwa zimene timafunikira pa moyo wathu wauzimu. (Mat. 24:45) Misonkhano yachigawo komanso misonkhano yathu yamkati mwa mlungu, ndi zina zomwe zimatitsimikizira zimenezi.

ONERANI VIDIYO YAKUTI LIPOTI LA KOMITI YOPHUNZITSA LA 2017, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Sitediyamu yodzaza ndi anthu omwe akuchita msonkhano

    Kodi ndani amene ayenera kulemekezedwa chifukwa cha misonkhano yachigawo ya pa nthawi yake yomwe timasangalala nayo, ndipo n’chifukwa chiyani?

  • Kodi ntchito yokonzekera msonkhano wachigawo imayamba liti?

  • Abale a m’dipatimenti yojambula mavidiyo akujambula vidiyo ya pamsonkhano

    Kodi nkhani za pamsonkhano wachigawo zimasankhidwa bwanji?

  • Kodi pamakhala ntchito yotani pokonza msonkhano wachigawo?

  • Kodi njira zophunzitsira ku sukulu ya Giliyadi zimagwiritsidwa ntchito bwanji pokonza misonkhano ya mkati mwa mlungu?

  • M’bale akuwerenga ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu

    Kodi madipatimenti osiyanasiyana amathandizana bwanji pokonza ndandanda yautumiki?

Kodi inuyo mumachita zotani poyamikira zinthu zauzimu zomwe Yehova amatipatsa?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani