MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Limbani Mtima Pamene Mapeto Akuyandikira
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI?: Posachedwapa padzikoli padzachitika zinthu zochititsa mantha ndipo tidzafunika kukhala olimba mtima komanso kusonyeza kuti timadalira kwambiri Yehova kuposa kale lonse. Chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuwonongedwa kwa zipembedzo zonyenga. (Mt 24:21; Chv 17:16, 17) Pa nthawi yovuta imeneyo, n’kutheka kuti tizidzalengeza uthenga wamphamvu wachiweruzo. (Chv 16:21) Gogi wa ku Magogi adzatiukira. (Eze 38:10-12, 14-16) Pofuna kuteteza anthu ake, Yehova adzayambitsa ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ (Chv 16:14, 16) Kuti tidzakhale olimba mtima kwambiri zimenezi zikamadzachitika, tikuyenera kukhala okhulupirika panopa tikamakumana ndi mayesero.
MMENE TINGACHITIRE ZIMENEZI:
Tiyenera kumatsatira mfundo zapamwamba za Yehova molimba mtima.—Yes 5:20
Tiyenera kupitirizabe kulambira Yehova limodzi ndi Akhristu anzathu.—Ahe 10:24, 25
Tiyenera kutsatira mwamsanga malangizo amene gulu la Yehova limatipatsa.—Ahe 13:17
Tiziganizira mmene Yehova anapulumutsira anthu ake m’mbuyomu.—2Pe 2:9
Tizipemphera komanso kudalira Yehova.—Sl 112:7, 8
ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI KUTSOGOLOKU TIDZAFUNIKA KULIMBA MTIMA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi n’chifukwa chiyani zinali zovuta kuti ofalitsa ena amvere malangizo a akulu mpingo wawo utagawidwa n’kuphatikizidwa ndi mipingo ina?
Kodi kulimba mtima kumagwirizana bwanji ndi kumvera?
N’chifukwa chiyani tidzafunika kulimba mtima pa Aramagedo?
Tizikonzekera panopa zinthu zimene zidzachitike m’tsogolo pomwe tidzafunike kulimba mtima
Kodi ndi nkhani iti ya m’Baibulo imene ingatithandize kulimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti Yehova adzatipulumutsa?—2Mb 20:1-24