MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Musamafalitse Nkhani Zabodza
Masiku ano, nkhani zimafalitsidwa mwamsanga komanso kwa anthu ambiri pogwiritsa ntchito zinthu monga nyuzipepala, wailesi, TV kapena intaneti. Atumiki a “Mulungu wachoonadi” safuna kufalitsa nkhani zabodza, ngakhale mosadziwa. (Sl 31:5; Eks 23:1) Nkhani zabodza zikanenedwa kwa anthu ena zingabweretse mavuto ambiri. Mukamafuna kudziwa ngati nkhani inayake ndi yoona kapena ayi, muzidzifunsa kuti:
‘Kodi nkhaniyi ndi yochokera kwa munthu kapena gulu lodalirika?’ N’kutheka kuti munthu amene wakuuzani nkhaniyo sakudziwa nkhani yonse. Nthawi zambiri nkhani zimasinthidwa zikamafalitsidwa ndi anthu. Choncho muzichita zinthu mosamala ngati simukudziwa kumene nkhaniyo yachokera. Anthu amene ali ndi udindo mumpingo ayenera kusamala kwambiri kuti asamafalitse nkhani zopanda umboni. Zili choncho chifukwa abale ndi alongo amakhulupirira zimene iwo amanena.
‘Kodi nkhaniyi ikhoza kuipitsa mbiri ya munthu wina kapena gulu lina?’ Ngati zimenezi zingachitike, si bwino kuuza anthu ena nkhaniyo.—Miy 18:8; Afi 4:8.
‘Kodi nkhaniyi ingachitikedi?’ Muzisamala kwambiri mukamva nkhani zokhudza zinthu zodabwitsa.
ONERANI VIDIYO YAKUTI, KODI NDINGATANI KUTI NDITHETSE MISECHE? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Malinga ndi Miyambo 12:18, kodi mawu angapweteke bwanji anthu?
Kodi lemba la Afilipi 2:4 limatithandiza bwanji kuona moyenera nkhani yolankhula za anthu ena?
Kodi tizichita chiyani anthu akayamba kunena zinthu zoipa zokhudza anthu ena?
Tisanayambe kulankhula za ena, kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati?