MOYO WATHU WACHIKHRISTU
‘Timakobidi Tiwiri Tating’ono’ Tamtengo Wapatali
Tindalama timene mayi wamasiye anapereka tinali tochepa kwambiri moti munthu sakanatha kugula nato ngakhale chakudya choti adye kamodzi kokha. (Onani w08 3/1 12 ¶1-3) Koma zimene anaperekazo zinasonyeza kuti ankakonda komanso kulemekeza zimene Yehova wakonza kuti anthu azimulambira. Chifukwa cha zimenezi, chopereka chake chinali chamtengo wapatali kwambiri kwa Atate wake wakumwamba.—Mko 12:43.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ‘MUZIPEREKA MPHATSO KWA YEHOVA,’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi zopereka zathu zimathandiza pa ntchito monga ziti?
N’chifukwa chiyani tinganene kuti zopereka zathu zimakhala zamtengo wapatali ngakhale zikuoneka zochepa?
Kodi tingadziwe bwanji zambiri zokhudza mmene tingaperekere ndalama?—Onani bokosi lakuti “Dziwani Zambiri Pawebusaiti Yathu”