MOYO WATHU WACHIKHRISTU
‘Muziika Kenakake Pambali’
Tisamapereke ndalama zothandizira pa ntchito za Ufumu mongodzidzimukira. M’malomwake, tizichita monga mmene Mtumwi Paulo anatilimbikitsira kuti, nthawi zonse ‘tiziika kenakake pambali.’ (1Ak 16:2) Tikamatsatira malangizo ouziridwawa, timakhala tikuthandiza pa kulambira koyera komanso timasangalala. Kaya zopereka zathu zikhale zochepa bwanji, Yehova amatiyamikira kwambiri chifukwa chofunitsitsa kumulemekeza ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.—Miy 3:9.
Kodi kupangiratu pulani ya ndalama zoti tikapereke n’kothandiza bwanji?
Kodi ena anachita zotani kuti ‘aziika kenakake pambali’?