Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb21.05 8
  • Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Mafanizo Abwino
    Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso
  • Muzilola Kuti Yehova Azikuthandizani Kudzera M’pemphero
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21.05 8
Mayi ndi mwana wake wamkazi akuyang’ana mbalame komanso maluwa pamene akumvetsera Ulaliki wa Paphiri wa Yesu.

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo

Tikamapanga maulendo obwereza kapena kuchititsa maphunziro a Baibulo, tiyenera kuthandiza amene tikuwaphunzitsawo kumvetsa mfundo zikuluzikulu. Tikamagwiritsa ntchito mafanizo pofotokoza mfundozi, timawafika pamtima komanso amazikumbukira mosavuta.

Mukamakonzekera ulendo wobwereza kapena phunziro la Baibulo, muzisankha mfundo zikuluzikulu, osati zing’onozing’ono, zomwe mukagwiritse ntchito mafanizo pozifotokoza. Kenako pezani mafanizo osavuta kumva omwe ndi ogwirizana ndi moyo wa tsiku ndi tsiku. (Mt 5:14-16; Mko 2:21; Lu 14:7-11) Mukamakonzekera, muziganizira zokhudza moyo komanso zimene munthuyo amachita. (Lu 5:2-11; Yoh 4:7-15) Mukaona munthuyo akusangalala chifukwa choti wamvetsa bwino mfundo yaikulu, inunso mudzasangalala.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​—MUZIGWIRITSA NTCHITO MAFANIZO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muziwonjezera Luso Lanu Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo.’ Jane akufunsa Anita funso.

    N’chifukwa chiyani ophunzira amafunika kuwathandiza kuti amvetse bwino mavesi a m’Baibulo?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muziwonjezera Luso Lanu Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo.’ Anita akuuza Jane fanizo.

    Kodi Anita anagwiritsira ntchito bwanji fanizo pofotokoza mfundo ya pa Aroma 5:12?

  • Chithunzi cha m’vidiyo yakuti ‘Muziwonjezera Luso Lanu Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muzigwiritsa Ntchito Mafanizo.’ Anita akuonetsa Jane vidiyo.

    Mafanizo abwino amafika anthu pamtima

    Kodi mafanizo abwino angathandize bwanji omvera athu?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kumagwiritsa ntchito mavidiyo komanso zinthu zina zophunzitsira zimene gulu la Yehova latipatsa tikakhala mu utumiki?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani