CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Yehova Amafuna Kuti Tizimulambira Bwanji?
Aisiraeli ankafunika kumvera, kukonda komanso kutumikira Yehova ndi mtima wonse komanso moyo wawo wonse (De 11:13; it-2 1007 ¶4)
Chilichonse chimene chinkagwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga chinkafunika kuwonongedwa (De 12:2, 3)
Aliyense ankafunika kumalambira Yehova pamalo amene Yehovayo anasankha (De 12:11-14; it-1 84 ¶3)
Yehova amafuna kuti anthu ake azimulambira ndi moyo wawo wonse, azikana kulambira konyenga komanso azikhala ogwirizana.