KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Muziwafika Pamtima
Kumvera Mulungu kumayambira mumtima. (Miy 3:1) Choncho mukamaphunzitsa anthu Baibulo, muziyesetsa kuwafika pamtima. Kodi mungachite bwanji zimenezi?
Musamangophunzitsa ophunzira anu mfundo za choonadi cha m’Baibulo, koma muziwathandiza kuona mmene mfundozo zikukhudzira moyo wawo komanso ubwenzi wawo ndi Yehova. Muziwathandiza kumvetsa bwino mmene mfundo za m’Baibulo zimasonyezera chikondi, ubwino, komanso chilungamo cha Mulungu. Mosamala komanso mokoma mtima, muziwafunsa mafunso omwe angawathandize kuganizira mmene akumvera chifukwa cha zimene akuphunzirazo. Athandizeni kudziwa mmene kusintha mmene amaganizira kapena kusiya khalidwe linalake loipa kungawathandizire. Mukaona munthu amene mukuphunzira naye Baibulo akukonda Yehova ndi mtima wonse, mudzakhala wosangalala kwambiri.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA—MUZIWAFIKA PAMTIMA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
N’chifukwa chiyani Anita anafunsa Jane kuti: “Unaganiziraponso zimene tinakambirana Monday?”
Kodi Anita anathandiza bwanji Jane kumvetsa kuti mfundo za m’Baibulo zimasonyeza kuti Yehova amamukonda?
Tikamayesetsa kuwafika pamtima anthu omwe timaphunzira nawo, zidzawalimbikitsa kuti apite patsogolo
Kodi Anita anathandiza bwanji Jane kuganizira mmene angasonyezere kuti amakonda Mulungu?