Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb21.09 10
  • Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira
  • Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muziwafika Pamtima
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Muzilola Kuti Yehova Azikuthandizani Kudzera M’pemphero
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
Onani Zambiri
Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
mwb21.09 10

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira

Yehova watipatsa zinthu zomwe zimatithandiza kuphunzitsa mwaluso monga mavidiyo, timapepala, magazini, timabuku, mabuku komanso Baibulo. (2Ti 3:16) Watipatsanso zinthu zofufuzira zomwe zimatithandiza kufotokoza Malemba momveka bwino. Zinthu zake ndi monga Watchtower Library, JW Library®, LAIBULALE YA PA INTANETI ndi Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani.

Mukamafufuza mfundo za m’Baibulo pogwiritsa ntchito zinthu zofufuzira zomwe tili nazo, mudzakhala osangalala kwambiri. Muziyesetsa kuphunzitsa ophunzira anu kudziwa mmene angagwiritsire ntchito zinthuzi, ndipo nawonso adzakhala osangalala akamapeza mayankho a m’Baibulo pawokha.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIGWIRITSA NTCHITO ZOMWE YEHOVA WATIPATSA KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​—MUZIGWIRITSA NTCHITO ZINTHU ZOFUFUZIRA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Zomwe Yehova Watipatsa Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira.” Jane akumufotokozera Anita kuti amakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha.

    Kodi Jane anatsutsa chiyani zokhudza chilengedwe?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Zomwe Yehova Watipatsa Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira.” Anita akugwiritsa ntchito “Buku Lofufuzira Nkhani” mfundo zokhudza chilengedwe.

    Kodi Anita anapeza kuti mfundo zokhudza nkhaniyo?

  • Chithunzi cha muvidiyo yakuti “Muzigwiritsa Ntchito Zomwe Yehova Watipatsa Kuti Muzisangalala Ndi Ntchito Yophunzitsa​—Muzigwiritsa Ntchito Zinthu Zofufuzira.” Anita akufotokozera Jane mosangalala zimene wapeza pamene amafufuza.

    Kufufuza komanso kuuza ena mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kukhala osangalala

    Kodi Anita anasankha bwanji mfundo zomwe zinali zothandiza kwa Jane?

  • Kodi kugwiritsa ntchito zinthu zofufuzira kunathandiza bwanji Anita?

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani